Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/06 tsamba 1
  • Tsanzirani Mulungu Wathu Wachisangalalo, Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Mulungu Wathu Wachisangalalo, Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Timalalikira Uthenga Wabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Yehova Amakonda Opatsa Mokondwerera
    Nsanja ya Olonda—1992
  • “Mulungu Akonda Wopereka Mokondwera”
    Imbirani Yehova Zitamando
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 7/06 tsamba 1

Tsanzirani Mulungu Wathu Wachisangalalo, Yehova

1 Yehova amafuna kuti anthu azisangalala. Mawu ake amatipatsa chiyembekezo cha madalitso abwino kwambiri amene wakonzera anthu. (Yes. 65:21-25) Ena ayenera kuona kuti timasangalala kugawana nawo ‘uthenga wabwino wa ulemerero wa Mulungu wachisangalalo.’ (1 Tim. 1:11, NW) Mmene timalankhulira uthenga wa Ufumu, ziyenera kusonyeza kuti timakonda choonadi ndiponso kuti tili ndi chidwi chenicheni ndi anthu amene timalankhula nawo.—Aroma 1:14-16.

2 N’zoona kuti nthawi zina n’zovuta kukhala wansangala. Izi zili choncho chifukwa chakuti m’magawo ena, ndi anthu ochepa chabe amene amalabadira uthenga wa Ufumu. Ndipo nthawi zina timakhala tikulimbana ndi mavuto athu. Kuti tipitirizebe kukhala achimwemwe, ndi bwino kuganizira mmene uthenga wa Ufumu ulili wofunika kwa anthu a m’gawo lathu. (Aroma 10:13, 14, 17) Kusinkhasinkha za zimenezi kudzatithandiza kupitirizabe kulengeza mwachimwemwe zinthu zimene Yehova wakonza kuti apulumutse anthu.

3 Yesetsani Kulankhula Kwambiri za Zinthu Zabwino: M’pofunikanso kukhala osamala ndi zinthu zimene timalankhula. Ngakhale kuti tingayambe kukambirana ndi anthu mwa kutchula mavuto kapena nkhani zina ndi zina zimene zili m’maganizo mwawo, tiyenera kupewa kumangolankhula za zinthu zoopseza mosaganizira bwino. Kumbukirani kuti ntchito yathu ndi yolalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Uthenga umenewu wazikidwa pa malonjezo a Mulungu a tsogolo labwino. (2 Pet. 3:13) Poganizira zimenezi, tiyeni tizigwiritsa ntchito Malemba kuti ‘timange osweka mtima.’ (Yes. 61:1, 2) Izi zingatithandize tonsefe kuti tipitirizebe kukhala achimwemwe ndi kutinso tizilankhula zinthu zabwino zokhazokha.

4 Tikamalalikira, zimakhala zoonekeratu kuti ndife anthu achimwemwe. Choncho, tiyeni tizitsanzira mtima wa Mulungu wathu wachisangalalo, Yehova, pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’gawo lathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena