Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/00 tsamba 8
  • Pemphani Thandizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pemphani Thandizo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • ‘Itanani Akulu’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • “Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 3/00 tsamba 8

Pemphani Thandizo

1 Mawu ouziridwa akuti “zoŵaŵitsa” ndithudi akunena za nthaŵi zathu zovutazi. (2 Tim. 3:1) Chotero, kodi mungachite chiyani pamene muli ndi mavuto auzimu amene simungathe kuwagonjetsa?

2 Kodi muli wofuna kulankhula ndi munthu wachikulire mwauzimu wa mumpingo? Ena anganyalanyaze kuchita zimenezi chifukwa cha manyazi, kusafuna kutopetsa ena, kapena kuganiza kuti palibe amene angawathandize. N’zoona kuti tiyenera kuyesetsa kusamalira maudindo athu mmene tingathere, koma tiyenera kumasuka kupempha thandizo pankhani zokhudza moyo wathu wauzimu.—Agal. 6:2, 5.

3 Poyambira: Mungafunike kulankhula ndi wopangitsa phunziro lanu la buku n’kumufunsa ngati mungayende naye mu utumiki wakumunda. Izi zidzakupatsani mpata womuuza chikhumbo chanu chofuna kukula mwauzimu. Ngati ndi mtumiki wotumikira, m’dziŵitseni zosoŵa zanu zofunika thandizo lauzimu ndipo adzapempha akulu kuti akuthandizeni. Kapena mungapite kwa aliyense wa akulu kumuuza nkhani zimene zikukudetsani nkhaŵa.

4 Kodi mukufuna thandizo lanji? Kodi pali chimene chafooketsa changu chanu? Kodi ndinu kholo limodzi lokha ndipo mukuyesetsa kuti ana anu akhale oyandikana ndi mpingo? Kodi ndinu munthu wachikulire wofunika thandizo? Kapena kodi pali mavuto ena amene akukubwezerani m’mbuyo? Kuchita zinthu m’nthaŵi zathu zovutazi n’kovuta—koma sikuti n’kosatheka. Thandizo lilipo.

5 Mmene Amuna Achikulire Amathandizira: Akulu amasamalira moona mtima. Adzamvetsera mavuto anu. Ngati ofalitsa ena ali ndi zopinga zimodzimodzizo, akulu adzalingalira zimenezi poweta ndi kuphunzitsa gulu. Monga “zitsanzo za gululo,” amakhala okonzeka kuti agwire nanu ntchito mwa chimwemwe. (1 Pet. 5:3) Kumvetsera abale achidziŵitso ameneŵa pamene akukamba mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kungapititse patsogolo utumiki wanu ndiponso kukuthandizani m’moyo wanu.—2 Tim. 3:16, 17.

6 Yesu watipatsa “mphatso [zambirimbiri] zokhala ndi amuna.” (Aef. 4:8, NW, mawu a m’munsi.) Izi zikutanthauza kuti akulu ndi ofunitsitsa kukuthandizani. Alipo kuti akuthandizeni. Kwenikweni iwo ‘ndi anu.’ (1 Akor. 3:21-23) Choncho m’malo momangika, lankhulani malingaliro anu momasuka. Pemphani thandizo limene mukufuna.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena