Kodi Ndinu Wofalitsa Ufumu Wokhazikika?
1 Tonse tinasangalala kumva kuti Malaŵi m’mwezi wa October 1999 inali ndi chiŵerengero chachikulu choposa ziŵerengero zina zonse cha ofalitsa okwanira 43,864. Ndithudi chinali chifukwa chogwirira ntchito pamodzi ndiponso mwakhama! Malinga ndi umboni umene ulipo, m’miyezi yotsatira, ena mwa ofalitsa ameneŵa akhala ndi vuto losakhala ofalitsa Ufumu okhazikika, popeza chiŵerengero cha maola pamwezi kuyambira nthaŵi imeneyo chakhala chapafupifupi 43,008. Izi zikusonyeza kuti m’modzi mwa ofalitsa 51 sapereka lipoti la muutumiki mwezi uliwonse. Tikukhulupirira kuti chilimbikitso chotsatirachi chingathandize kuthetsa vutoli.
2 Yamikirani Mwayiwu: Tiyenera kuyamikira kwambiri mwayi umene tili nawo wouza ena uthenga wabwino wa Ufumu. Ntchito imeneyi imakondweretsa mtima wa Yehova ndipo imathandiza anthu oona mtima kuphunzira njira yakumoyo. (Miy. 27:11; 1 Tim. 4:16) Kulalikira mokhazikika kumakulitsa luso lathu la muutumiki ndipo zimenezi zimatipatsa chimwemwe ndiponso zotsatira zabwino.
3 Perekani Lipoti la Ntchito: Ena amene amaloŵa muutumiki wakumunda amanyalanyaza kupereka lipoti la ntchito yawo panthaŵi yake. Tisayese n’komwe kuganiza kuti zimene tachita n’zosati n’kuchita kuperekera lipoti. (Yerekezani ndi Marko 12:41-44.) Zivute zitani, tiyenera kupereka lipoti la zimene tachita! Mwa kukhala ndi chizoloŵezi kunyumba, monga kugwiritsa ntchito kalendala kulembapo nthaŵi imene tathera muutumiki chidzakhala chotikumbutsa nthaŵi zonse kupereka lipoti lolondola mofulumira kumapeto a mwezi uliwonse.
4 Perekani Thandizo Lofunika: Mwina makonzedwe a pampingopo othandiza anthu ofuna kuthandizidwa kuti aziloŵa muutumiki nthaŵi zonse afunika kuwongolera. Mlembi wampingo ndi ochititsa maphunziro a Buku ayenera kupanga makonzedwe akuti ofalitsa ozoloŵera athandize. Ngati muli ndi ana kapena ophunzira Baibulo amene ali ofalitsa osabatizidwa, aphunzitseni kupereka malipoti awo mwezi uliwonse.
5 Kumbukirani nkhani yopezeka mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1997, ya mutu wakuti “Woyamikira Chifukwa Chotumikira Yehova Nthaŵi Yaitali.” Mlongo Ottilie Mydland wa ku Norway anakhala wofalitsa wokhazikika wauthenga wabwino asanabatizidwe mu 1921. Patatha zaka 76, ali ndi zaka 99, iye anati: “Ndili wosangalala kuti ndikukwanitsabe kukhala wofalitsa wokhazikika.” Kwa atumiki a Yehova onse, chimenechitu n’chitsanzo chabwino zedi chofunika kutsanzira!