Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/02 tsamba 8
  • Kodi Mumathandiza Kuti Lipoti Likhale Lolondola?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumathandiza Kuti Lipoti Likhale Lolondola?
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Njira Zimene Oyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo Amasonyezera Kuganizira Ena
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Ndinu Wofalitsa Ufumu Wokhazikika?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 12/02 tsamba 8

Kodi Mumathandiza Kuti Lipoti Likhale Lolondola?

1 Nkhani zambiri za m’Baibulo zili ndi manambala enieni, zimene zimathandiza anthu kukhala ndi chithunzi chenicheni cha zimene zinachitika. Mwachitsanzo, Gideoni anagonjetsa Amidyani ndi anthu 300 okha. (Ower. 7:7) Mngelo wa Yehova anapha asilikali Aasuri 185,000. (2 Maf. 19:35) Pa Pentekoste wa m’chaka cha 33 C.E., anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa, ndipo patangopita nthaŵi pang’ono anthu okhulupirira anachuluka mpaka pafupifupi 5,000. (Mac. 2:41; 4:4) Pa zimenezi, n’koonekeratu kuti atumiki a Mulungu akale ankayesetsa kulemba nkhani bwinobwino ndiponso molondola.

2 Masiku ano gulu la Yehova limatilangiza kuti mwezi uliwonse tizipereka malipoti a ntchito yathu ya utumiki wa kumunda. Kumvera kwathu mokhulupirika dongosolo limeneli kumathandiza kuti ntchito yolalikira iyang’aniridwe bwino. Malipoti angasonyeze kuti mbali ina ya utumiki ikufunika kuisamalira kapena kuti m’gawo lina kukufunika antchito ambiri. Malipoti a utumiki wa kumunda amathandiza akulu pampingo kudziŵa anthu amene angachite zambiri mu utumiki wawo komanso amene akufunika kuwathandiza. Ndiponso malipoti osonyeza kuti ntchito yolalikira Ufumu ikuyenda bwino, amalimbikitsa Akristu anzathu onse. Kodi mukuchita mbali yanu kuti lipoti likhale lolondola?

3 Udindo Wanu: Kodi pamapeto pa mwezi zimakuvutani kukumbukira zimene mwachita mu utumiki? Ngati zimakuvutani, bwanji osamalemba zimene mwachita nthaŵi iliyonse imene mwaloŵa mu utumiki wa kumunda? Ena amalemba zimenezi pa kalendala kapena m’kope lolembamo. Ena amatenga kapepala kolembapo lipoti la utumiki wa kumunda. Pamapeto pa mwezi, perekani mwamsanga malipoti anu kwa woyang’anira phunziro lanu la buku. Kapena ngati mukufuna, mungakaike malipoti anu m’kabokosi ka malipoti pa Nyumba ya Ufumu. Ngati mwaiŵala kubweretsa malipoti anu, muuzeni mwamsanga woyang’anira phunziro lanu la buku kuti muperekabe, musadikire kuti akukumbutseni. Kusamala kwanu polemba malipoti a ntchito yanu kumasonyeza kulemekeza dongosolo la Yehova ndiponso kuganizira ndi kukonda abale amene apatsidwa ntchito yotolera ndi kuwonkhetsa malipoti.—Luka 16:10.

4 Udindo wa Woyang’anira Phunziro la Buku: Popeza woyang’anira phunziro la buku ndi mbusa woganizira ena, amachita chidwi ndi zimene gulu lakelo lachita mwezi wonse. (Miy. 27:23) Amadziŵa ngati wofalitsa aliyense akuchita utumiki mokhazikika, mokwanira, ndiponso mosangalala ndipo amathandiza mwamsanga ngati wina watha mwezi wonse osaloŵa mu utumiki. Nthaŵi zambiri zimene zimafunika n’kungom’limbikitsa, kumuuza mfundo yothandiza kapena kum’pempha kuti ayende nanu limodzi mu utumiki wa kumunda.

5 Pamapeto pa mwezi, woyang’anira phunziro la buku azionetsetsa kuti onse m’gulu lake akwaniritsa udindo wawo wopereka malipoti a ntchito yawo kuti mlembi azipereka ku ofesi ya nthambi lipoti la mpingo lolondola pasanafike pa sikisi mwezi winawo. Mwezi ukamatha, zingamuthandize kukumbutsa gululo kupereka malipoti ndiponso akhale ndi mapepala olembapo malipoti pamalo a phunziro la bukuwo. Ngati ena amaiŵalaiŵala kupereka lipoti la ntchito yawo, aziwakumbutsa ndiponso aziwalimbikitsa moyenera.

6 Kupereka mwamsanga malipoti a utumiki wathu wa kumunda kumathandiza kuti lipoti likhale losonyezadi zimene zinachitika m’munda. Kodi mudzachita mbali yanu mwa kupereka mwamsanga lipoti la ntchito yanu mwezi uliwonse?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena