Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kupereka pemphero pamisonkhano yampingo?
Pemphero la mpingo ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwathu. Kuimira ena kwa Yehova ndi mwayi waukulu kwabasi ndiponso ndi udindo waukulu. Chifukwa cha kufunika kwake, akulu ayenera kulingalira bwino posankha mbale amene akuyenerera kupereka pemphero pamisonkhano. Abale obatizidwa oimira mpingo m’pemphero ayenera kukhala atumiki okhwima achikristu azitsanzo zabwino ndiponso amene amalemekeza mpingo. Mapemphero awo odzichepetsa ndi aulemu ayenera kusonyeza unansi wabwino ndi Yehova Mulungu. Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1986 yakuti, “Praying Before Others With a Humble Heart” (Kuimira Ena M’pemphero ndi Mtima Wodzichepetsa) ili ndi mfundo zofunika zimene zili zothandiza kwambiri makamaka kwa awo amene amapemphera poyera m’malo mwa mpingo.
Akulu sadzasankha mbale amene ali wokayikitsa kapena wakhalidwe lachibwana kupereka pemphero. Mbale amene amaoneka wosasangalala kapena amene amafuna kugwiritsa ntchito pemphero la poyera monga ponenera zofooka za anzake sangasankhidwe. (1 Tim. 2:8) Ngakhale ngati mbale wachinyamata ali wobatizidwa, akulu ayenerabe kuona ngati iye ali wokhwima mwauzimu kwakuti n’kuimira mpingo mpemphero.—Mac. 16:1, 2.
Nthaŵi zina pamisonkhano ya utumiki wakumunda, kungakhale kofunika kuti mlongo wobatizidwa apereke pemphero ngati palibe mbale woyeneretsedwa kuti aimire gululo. Mkaziyo ayenera kuvala duku labwino. Ngati n’zodziŵikiratu kuti mbale woyeneretsedwa sadzakhalapo pa misonkhano ina yokonzekera utumiki, akulu ayenera kuuza mlongo woyeneretsedwa kuti atsogolere.
Kaŵirikaŵiri tcheyamani wa Msonkhano Wapoyera ndi amene amapereka pemphero lotsegulira. Komabe, pamisonkhano yampingo ina, pamene pali abale oyeneretsedwa angapo, mbale wina osati amene watsegulira msonkhano kapena amene wakamba mbali yomaliza angapemphedwe kupereka pemphero lotsegulira kapena lomaliza. Mulimonse mmene zingakhalire, mbale amene wapemphedwa kuti apereke pemphero pamsonkhano wampingo ayenera kuuzidwiratu kuti athe kulingalira zimene ati akanene. Chotero akhoza kupereka pemphero lomveka, logwira mtima lomwe lili loyenera pamsonkhano umenewo.
Mapemphero amenewo sayenera kukhala aatali. Pamene mbale akupereka pemphero lapoyera, nthaŵi zambiri amamveka bwino ngati waimirira, kulankhula ndi mawu okweza bwino, ndiponso kulankhula zomveka. Izi zidzachititsa kuti onse osonkhana amve pempherolo ndipo pomaliza pake anene kuti “Amen!”—1 Mbiri 16:36; 1 Akor. 14:16.