Miyoyo Ili Pachiswe!
1 Baibulo limanena momveka bwino kuti chifuno cha Yehova n’chakuti “anthu onse apulumuke.” Komanso, n’zoona kuti chiyembekezo cha moyo cha anthu miyandamiyanda a padziko lapansi chimadalira pa mmene amaonera Yehova Mulungu ndi Ufumu wake mwa Yesu Kristu. “Chidziŵitso cholondola cha choonadi” ndicho maziko okha a malingaliro abwino. (1 Tim. 2:3, 4, NW) Kuwonjezera pa kuchenjeza kuti posachedwapa anthu oipa onse adzachotsedwa m’dziko n’cholinga choti dziko lapansi latsopano lolungama la Mulungu liloŵe m’malo, tatumidwa kuti tigwirenso ntchito yofunika kwambiri yopulumutsa miyoyo.—Mat. 24:14; 28:19, 20; Aroma 10:13-15.
2 N’chifukwa Chiyani Ili Yofunika Kwambiri? Yesu anachenjeza za “masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko.” (Mat. 24:21) Masautso ameneŵa adzafika pakaindeinde pa Armagedo. (Chiv. 16:16) Namtindi wa anthu amene adzawonongedwe akapanda kulabadira uthenga wabwino ndi anthu monga abale athu osakhulupirira, anansi athu, ogwira nawo ntchito, anzathu akusukulu, ndi anzathu ena. Koma motsanzira Mulungu, amene anasonyeza chikondi kwa anthu apadziko lonse mwa kupereka Mwana wake, Yesu Kristu, monga dipo la anthu onse, cholinga chathu ndi chofikira “anthu onse.” (Yoh. 3:16) Tiyenera kuyesetsa mwachangu kuuza anthu onse kuthaŵira ku malo a Mulungu achisungiko. Mwa kugwira ntchito yolalikira mokwanira, sitingakhale ndi mlandu wa mwazi.—Ezek. 33:1-7; 1 Akor. 9:16.
3 Kodi Cholinga Chathu N’chiyani? Mawu onse a Mulungu amagogomezera kufunika kwa ntchito yolalikira. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera, “chikondi cha Kristu chitikakamiza” kukhala mogwirizana ndi njira za Mulungu. (2 Akor. 5:14) Komanso, nthaŵi zambiri Nsanja ya Olonda imagogomezera ntchito yathu yolalikira. Nthaŵi zonse Utumiki Wathu wa Ufumu umapereka malangizo a mmene tingagwirire ntchito yathu yolalikira. Akulu amalinganiza ntchito ndiponso amatilimbikitsa kutengamo mbali m’ntchitoyo. Ofalitsa anzathu amatipempha kuti tiyende nawo muutumiki. Timamva zochuluka ponena za mmene tingachitire ulaliki wathu, kugaŵira magazini ndi mabuku ena, kupanga ulendo wobwereza, kuchititsa maphunziro a Baibulo, ndi kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuchitira umboni. Zonsezi zimatithandiza kuti tikwaniritse cholinga chopulumutsa miyoyo.—1 Akor. 9:22, 23; Aef. 1:13.