Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/00 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 11
  • Mlungu Woyambira September 18
  • Mlungu Woyambira September 25
  • Mlungu Woyambira October 2
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 9/00 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 11

Nyimbo Na. 139

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 15: “Madalitso a Yehova Amatilemeretsa.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Nkhani Zochitika Posachedwapa Kuti Mudzutse Chidwi.” Kukambirana ndi omvetsera ndiponso zitsanzo. Tchulani nkhani zingapo zimene zangochitika posachedwapa zimene zachititsa anthu chidwi m’deralo. Kodi zimenezi zabweretsa nkhaŵa yotani ponena za m’tsogolo? Mogwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, tsamba 14, perekani malingaliro ena a mmene tingakonzere mawu oyamba omwe angathere m’kukambirana za m’Baibulo. Chitani zitsanzo zothandizadi ziŵiri ndiponso zokonzekeredwa bwino.

Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 18

Nyimbo Na. 2

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pendani mfundo zazikulu pa lipoti lampingo la chaka chautumiki cha 2000. Yamikirani zinthu zabwino zimene mpingo unachita. Tchulani mbali zimene zikufunika kuwongolera. Fotokozani mmene mpingo wachitira pa kupezeka pamisonkhano, kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo, ndiponso kuloŵa mokhazikika muutumiki wakumunda. Nenani zolinga zotheka m’chaka chimene chikubwerachi.

Mph. 20: “Miyoyo Ili Pachiswe!” Kukambirana ndi omvetsera. Gogomezerani malemba opezeka m’nkhaniyi.

Nyimbo Na. 30 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 25

Nyimbo Na. 93

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a September. Pendani Bokosi la Mafunso.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 15: Magazini Athu Samatha Ntchito. Kodi magazini akale a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akaunjikana mumatani nawo? Ofalitsa ena amataya magaziniwo, akumaganiza kuti nkhani zake zatha ntchito. Komano, Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1993 tsamba 3, unatilimbikitsa kutenga magazini ena akale n’kuwagaŵira pamene pali poyenera. Mungasankhe nkhani zapanthaŵi yake zimene zingasangalatse amuna, akazi, ogwira ntchito, okalamba, ndiponso achinyamata; ndiyeno n’kukhala ndi magaziniwo pafupi kuti muwagaŵire mpata ukapezeka. Sonyezani mmene tingasankhire nkhani komanso zimene tingachite pogaŵira magaziniwo. Simbani zokumana nazo zabwino zimene ofalitsa apeza pogaŵira magazini akale.

Nyimbo Na. 115 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 2

Nyimbo Na. 169

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Dziŵitsani mpingo za kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 kwapadera kumene kwakonzedwa, komwe kudzayamba Lolemba, pa October 16, ndipo kudzapitirira mpaka Lachisanu, pa November 17. Pemphani onse, kuphatikizapo ana ndi atsopano omwe, kudzatengamo mbali mokwanira. Ochititsa maphunziro a buku ayenera kuyamba pakalipano kulimbikitsa ndi kukonzekeretsa onse a m’gulu lawo kudzachita nawo mwachangu mmene angathere. Phatikizanipo zokumana nazo zolimbikitsa kuchokera m’kugaŵira Uthenga wa Ufumu kwa papitapo.

Mph. 20: “Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi—Mbali Yoyamba: N’kotheka.” Fotokozani chifukwa chake kuli kofunika kuthandiza ana. Kambiranani mmene tingagwiritsire ntchito uphungu wopezeka pa Deuteronomo 6:6, 7.

Mph. 15: Zokumana Nazo Poyambitsa Kukambirana. Mu pulogalamu ya Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyambira September 11, anati ndi bwino kuti muutumiki tiziyamba ndi nkhani zochitika posachedwapa pofuna kudzutsa chidwi ndiponso kuyamba kukambirana. Pemphani omvetsera kusimba zotsatira zabwino zimene akusangalala nazo mpaka pano chifukwa chakuti anagwiritsa ntchito malangizo ameneŵa.

Nyimbo Na. 205 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena