Chitani Zabwino Ndipo Mudzatamandidwa!
1 “Sindinaone anthu abata ngati ameneŵa.” “N’kosangalatsa kukhala nawo.” N’zimene anthu ambiri otiona ananena pamapeto a msonkhano wachigawo wachaka chatha, kusonyeza khalidwe labwino limene tili nalo monga gulu. (Miy. 27:2; 1 Akor. 4:9) Kwenikweni, satamanda ife koma Yehova. (Mat. 5:16) Nthaŵi yabwinonso kutamanda Mulungu ikutidikira pa Msonkhano Wachigawo wachaka chino wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.”
2 Chaka n’chaka amatikumbutsa mwachikondi za khalidwe labwino pa msonkhano wachigawo. N’chifukwa chiyani amatikumbutsa? Chifukwa pamene maganizo, kavalidwe, ndi khalidwe la dzikoli likuipiraipirabe, ife sitifuna kutengera zochita zake. Sitikufuna kudetsa mbiri yathu yabwinoyi. (Aef. 2:2; 4:17) Tikumbukiretu malangizo awa.
3 Chitani Zabwino pa Msonkhano: Kwapezeka kuti anthu ena samvera akalinde komanso sawalankhula mwachikristu. Sibwino kuona abale ndi alongo akuthamanga ndiponso kukankha anzawo pofuna kutenga mabuku kapena pofuna malo okhala “abwino.” Ndithudi, kudzikonda sikuzindikiritsa munthu kukhala wochita zabwino, komanso sikulemekeza Yehova Mulungu. Chotero tikhale achikondi, oleza mtima, ndiponso omvera.—Agal. 5:22, 23, 25.
4 Nthaŵi zambiri tikasonkhana pa misonkhano yachigawo anthu akudziko amaona ukhondo ndi udongo wathu. Umu ndi mmene ziyenera kukhalira chifukwa sitili “a dziko lapansi.” (Yoh. 17:14, 16) Makolo aziyamba kuphunzitsa ana awo kukhala audongo akadali aang’ono.
5 Kodi mumamva bwanji mukaona mapepala, mapulasitiki, makoko a malalanje ndi a nthochi, zitsekerero, ndi zina zotero zitatayidwa pabwalo lamsonkhano? N’zoona kuti zinthu zonsezi n’zofunika kutola kukataya m’mabini kapena m’khuti. Inde, oyang’anira msonkhano amakhala ndi Dipatimenti Yoyeretsa malo ya antchito odzifunira amene amasangalala kuthandiza kuti malo akhale oyera ndi audongo. Koma izi n’zinthu zimene TONSE tingathandize. Makolo, khalani chitsanzo kwa ana anu mwa kusataya kanthu pabwalo lamsonkhano. Ikani zinyalala zonse m’malo oyenera. Ndiyeno limbikitsani ana anu kuchita chimodzimodzi. Makomiti ena amsonkhano akonza zikwangwani zolembedwa kuti: “Mukaona chinyalala pansi, tolani!” Bwanji osadzachita zimenezi pabwalo lamsonkhano mukaona chinthu chimene sichili pamalo ake? Onse opezeka pamsonkhanopo adzayamikira kwambiri thandizo limeneli, makamaka, tidzasangalatsa Yehova, Mulungu wathu.—Miy. 27:11.
6 Mbali Yofunika Kuisamalira Kwambiri: Tikuganiza kuti mukudziŵa zoti pamsonkhano pakakhala madzi pamakhalanso vuto. Sizovuta madzi kutayikira pamalowo ndiponso kutereretsa n’kugwetsa ena. Anthu a mu Dipatimenti Yoyeretsa malo sangathetse vuto limeneli. Choncho tikupempha onse kuti asamataye madzi pafupi ndi pamene mukutungapo madzi. Komanso titapanda kusamala, m’zimbudzi mungataikire madzi ambiri. Ana aang’ono akafuna kupita kuchimbudzi, makolo aziwaperekeza ndiponso aziwaphunzitsa mmene angagwiritsire ntchito zimbudzi kuti zizikhala zaukhondo ndi zaudongo. Choncho, monga tikuonera, aliyense ali ndi udindo pankhani yaukhondo. Ngati ndife kholo, tili ndi udindo wina wophunzitsa ana athu kukhala aukhondo. Kusamalira nkhani yaukhondo kudzasonyeza kuti tikufunitsitsa kukhala m’dziko loyeretsedwa ndipo tidzakwanitsa miyezo ya ukhondo yofunika m’dziko latsopano.
7 Chitani Zabwino mwa Kuvala ndi Kudzikongoletsa Kwanu: Chaka chatha msonkhano wina wachigawo utatha, wolemba nyuzipepala ina yotchuka anati: “Chochititsa chidwi kwambiri chinali khalidwe la Mboni. Zinali zabwino zedi kuona anthu ambiri aulemu ndi odzilemekeza. Atavala zovala zabwino kwabasi za Lamlungu, mabanja ambiri osiyana mitundu komanso chikhalidwe analoŵa m’bwalo mwakachetechete. Khalidwe lawo n’losiyana kwambiri ndi la anthu ambiri amene amadzaza m’bwalolo. Ndipo, Mboni zimasiyana kwambiri ndi anthu ena onse. N’zofala kwambiri kuona magulu opulupudza. . . . Ndithudi, gulu la Mboni n’losangalatsa.” Zovala zathu ndiponso kudzikongoletsa kwathu kapena khalidwe lathu lisadodometse mwanjira iliyonse mkhalidwe wauzimu wa pamalo amsonkhano.—Afil. 1:10; 1 Tim. 2:9, 10.
8 Chitani Zabwino pa Ubatizo: Okabatizidwa afunika kulemekeza kwambiri mwambo umenewu. Kuvala zovala zosambira zabwino kudzasonyeza kuti akuzindikira kupatulika kwa mwambowu. N’kopindulitsa kwambiri ochititsa maphunziro a Baibulo kupenda pamodzi ndi ophunzira awo “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, asanapite kumsonkhano wachigawo.
9 Bata ndiponso khalidwe lathu laumulungu limasonyeza zikhulupiriro zathu zachikristu ndipo anthu oona mtima savutika kuzindikira choonadi. Chotero, pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” tipitirize ‘kuchita zabwino’ ndipo tidzatamandidwa.—Aroma 13:3.