Khalidwe Lathu Labwino Limalemekeza Mulungu
1. Pa nthawi ya msonkhano wachigawo, n’chifukwa chiyani anthu ambiri savutika kuzindikira kuti tili ndi msonkhano?
1 Tikamachita msonkhano wachigawo, anthu savutika kuzindikira zimenezo. Nthawi zambiri misonkhano yathu ikamachitikira m’mizinda, nyuzipepala komanso ofalitsa nkhani amalemba nkhani zokhudza misonkhanoyi. Nthawi zambiri malesitanti amakhala odzaza ndi anthu amene abwera ku msonkhano wachigawo. Ndipo anthu okhala m’madera amene kukuchitikira msonkhanowo, amaona alendo ambiri atavala mabaji a msonkhano. M’munsimu muli mfundo zothandiza, zotikumbutsa zoyenera kuchita kuti tidzalemekeze Mulungu chifukwa cha khalidwe lathu labwino pamene tikuchita msonkhano wachigawo.—1 Pet. 2:12.
2. Kodi tingalemekeze bwanji Mulungu tikavala modzilemekeza pamene tili ku msonkhano wachigawo?
2 Valani Modzilemekeza: N’zoona kuti tikakhala pa msonkhano timayenera kuvala modzilemekeza. Komabe, tiyeneranso kuvala modzilemekeza ngakhale pamene sitili pamalo a msonkhano. Kuvala modzilemekeza tikapita kulesitanti, pogula zinthu ndiponso pochita zinthu zina, kumachititsa chidwi anthu otiona. Ngakhale kuti tikakhala m’malo amenewa sitifunikira kuchita kuvala ngati tili pamsonkhano, komabe tiyenera kuvala zoyenera komanso modzilemekeza. Anthu azitha kutisiyanitsa mosavuta ndi anthu ena amene satumikira Yehova. (Aroma 12:2) Komanso, tiyenera kuvala mabaji a msonkhano. Zimenezi zidzapangitsa kuti anthu adziwe za msonkhano wathu ndipo zidzatipatsa mwayi wowalalikira. Kuvala mabaji kudzathandizanso anthu amene abwera ku msonkhanowu kuti atizindikire mosavuta.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odekha komanso oganizira ena?
3 Khalani Odekha Komanso Oganizira Ena: M’dzikoli, anthu ambiri ndi odzikonda komanso osayamika. (2 Tim. 3:1-5) Koma ifeyo tidzayesetse kukhala odekha komanso oganizira ena. Zimenezi zidzakhala zothandiza kwambiri kwa anthu otiona monga ogwira ntchito m’malesitanti. Posunga malo kapena kulandira mabuku ndi zinthu zina zomwe zidzatuluke pa msonkhanowu, tisadzachite zinthu zongofuna kudzipindulitsa koma zopindulitsanso ena. (1 Akor. 10:23, 24) Munthu wina atapezeka pa msonkhano kwa nthawi yoyamba, ananena kuti: “Sindikumbukira nkhani iliyonse imene inakambidwa pa tsikulo, koma zimene sindidzaiwala ndi khalidwe labwino la Mboni.”
4. Ngati n’zotheka kwa ife, n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zothandiza nawo pa ntchito zosiyanasiyana pa msonkhano wachigawo wa chaka chino?
4 Anthu Ogwira Ntchito Mongodzipereka: Akhristu oona amadziwika kuti ndi anthu odzipereka. (Sal. 110:3) Kodi inuyo mungadzathandize nawo kugwira ntchito zosiyanasiyana pa msonkhano wa chaka chino? Pa nthawi ya msonkhano wina, abale ndi alongo pafupifupi 600 anadzipereka kuyeretsa malo amene panachitikira msonkhano, msonkhanowo usanachitike. Anthu ogwira ntchito pamalowo anagoma ndi zimene anaona, ndipo ananena kuti: “Zoterezi sitinazionepo. N’zovuta kukhulupirira kuti anthu onsewa angodzipereka kudzagwira ntchito imeneyi.” Tikuyembekezera mwachidwi misonkhano yachigawo ya 2013. Sikuti pa misonkhanoyi tidzangokhala ndi mwayi womvetsera komanso kuphunzitsidwa ndi Yehova, koma tidzakhalanso tikulemekeza Mulungu.
[Box on pages 3-6]
Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2013
◼ Nthawi ya Msonkhano: Masiku onse atatu, msonkhano uzidzayamba ndi nyimbo zomvetsera pa nthawi ya 8:20 m’mawa. Nyimbozi zikayamba, tonse tiyenera kudzakhala pamalo athu kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Lachisanu ndi Loweruka msonkhano udzatha 3:55 madzulo. Lamlungu, msonkhano udzatha nthawi ya 2:45 madzulo.
◼ Koimika Magalimoto: Pamalo onse ochitira msonkhano padzakhala malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto adzaonetsetse kuti zitseko za magalimoto ndi zokhoma. Nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.
◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi komanso anthu amene panopa tikuphunzira nawo Baibulo.—1 Akor. 13:5.
◼ Chakudya Chamasana: Tikulimbikitsidwa kuti tidzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya pa nthawi yopuma. Mungatenge zakudya monga tchipisi, mpunga wophika, mbatata, chinangwa ndi zakumwa. Koma mowa si wololedwa pamalo a msonkhano.
◼ Zopereka: Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu popereka mwaufulu ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Polemba macheke, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku “Association of Jehovah’s Witnesses of Malawi.”
◼ Ngozi Ndiponso Matenda Adzidzidzi: Ngati munthu wadwala mwadzidzidzi pa msonkhanopo, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo aone mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.
◼ Mankhwala: Ngati mumamwa mankhwala enaake, muyenera kuonetsetsa kuti mwatenga okwanira chifukwa mankhwala amene mumamwawo sadzapezeka pa msonkhano. Anthu amene amadzibaya mankhwala a matenda a shuga ayenera kusamala mmene angataire masilenji. Sayenera kutaya m’mabini a pamalo a msonkhano kapenanso kungotaya pamene akhala.
◼ Ovutika Kumva: Pulogalamu ya msonkhano idzamasuliridwa m’chinenero chamanja m’malo otsatirawa: Blantyre, Kasungu, Lilongwe, Luchenza, Magawa, Mangochi, Mzuzu, Nkhata Bay, Songani ndi malo enanso. Pa tsiku loyamba la msonkhanowu padzakhala chilengezo chonena za zimenezi.
◼ Perefyumu: Poganizira anthu amene, chifukwa cha mavuto ena, amadana ndi fungo lamphamvu, ndi bwino kusagwiritsa ntchito perefyumu wamphamvu kwambiri.—1 Akor. 10:24.
◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira mawu ku magetsi kapena kuzokuzira mawu za pamsonkhano ndipo mudzasamale kuti zisasokoneze ena.
◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli m’kati.
◼ Foni za M’manja: Muyenera kuzitchera kuti zisalire, n’kusokoneza ena.
◼ Mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43): Ngati pa nthawi ya msonkhano munalalikira kwa munthu wachidwi, mungalembe zokhudza munthuyo pa fomu ya Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako ku msonkhanowo.
◼ M’malesitanti: Khalidwe lathu liyenera kulemekeza dzina la Yehova tikakhala mulesitanti. Tiyenera kuvala zovala zoyenera Mkhristu.
◼ Utumiki Wodzipereka: Misonkhano yachigawo imakhala yosangalatsa. Koma mukhozanso kusangalala kwambiri ngati mungadzipereke kugwira nawo ntchito zina ndi zina za pa msonkhanowu. (Mac. 20:35) Ngati mukufuna kudzachita nawo utumikiwu, uzani abale a ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka. Ana osafika zaka 16 angachite nawo utumiki umenewu moyang’aniridwa ndi makolo awo kapena munthu wina wachikulire wovomerezedwa ndi makolowo.