Ndinu “Choonetsedwa”!
1 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Takhala ife choonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.” (1 Akor. 4:9) Kodi zimenezi zikutanthauzanji, ndipo kodi ziyenera kutikhudza motani mu utumiki wathu lerolino?
2 Mosakayikira mawu akuti “choonetsedwa” anakumbutsa Akorinto zimene zinkachitika kumapeto kwa maseŵera a Aroma, pamene anthu olakwa asanaphedwe mwankhanza ankawadutsitsa kutsogolo kwa khamu loonerera. Mofananamo, namtindi wa anthu ndi wa angelo unkaona momwe Akristu oyambirira ankazunzikira chifukwa cholalikira Ufumu. (Aheb. 10:32, 33) Kukhulupirika kwawo kunakhudza mitima ya anthu ambiri amene ankaona zimenezi zikuchitika, monga momwe kupirira kwathu kumachitira masiku ano. Kodi ndife choonetsedwa kwa ndani?
3 Ku Dziko Lapansi ndi kwa Anthu: Nthaŵi zina olemba nkhani amalemba zochita za anthu a Yehova. Timayamikira akafalitsa mbiri yabwino ndiponso yoona yokhudza ntchito yathu, koma nthaŵi zina timayembekezanso adani athu kufalitsa mbiri yoipa. Komabe, tipitirize kudzitsimikizira tokha monga atumiki a Mulungu “mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino.” (2 Akor. 6:4, 8) Anthu oona mtima savutika kuona kuti ndife ophunzira oona a Yesu Kristu.
4 Kwa Angelo: Zolengedwa zauzimu nazonso zimationa. Mdyerekezi ndi ziwanda zake amationerera koma ndi “udani waukulu,” akumafuna kuthetsa ntchito ‘yochitira umboni wa Yesu.’ (Chiv. 12:9, 12, 17) Angelo a Mulungu okhulupirika amaona ndipo amasangalala munthu wochimwa mmodzi akatembenuka. (Luka 15:10) N’zolimbikitsa kuti angelo amaona utumiki wathu monga ntchito yofunika mwachangu ndi yopindulitsa kwambiri imene ikuchitika padziko lapansi masiku ano!—Chiv. 14:6, 7.
5 Mukakumana ndi chitsutso kapena mukaganiza kuti utumiki wanu sukuphula kanthu, muzikumbukira kuti maso a anthu onse ali pa inu. Kupirira kwanu kumanena zambiri. Mapeto ake, “nkhondo [yanu] yabwino ya chikhulupiriro” idzakutheketsani ‘kugwira moyo wosatha.’—1 Tim. 6:12.