Pulogalamu ya Tsiku la Msonkhano Wapadera wa 2010
1. (a) Kodi ndi mitu yochokera m’Malemba yotani ya tsiku la msonkhano wapadera imene takhala nayo m’mbuyomu? (b) Kodi pali mfundo zina zimene munamva pa masiku a misonkhano yapadera ya m’mbuyomu zomwe zakuthandizani mu utumiki?
1 “Mutsimikizire Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti,” “Kuchirimika Monga Gulu Limodzi la Nkhosa,” “Pitirizani Kuchitira Umboni Choonadi,” “Ndife Dongo, Ndipo Yehova Amatiumba Ngati Mbiya.” (Afil. 1:9, 10, 27; Yoh. 18:37; Yes. 64:8) Imeneyi ndi ina mwa mitu ya masiku a misonkhano yapadera ya m’mbuyomu. Kodi mukufunitsitsa kudzapezeka pa tsiku la msonkhano wapadera m’chaka chautumiki cha 2010? Mutu wake udzakhala wakuti: “Nthawi Yotsalayi Yafupika,” ndipo wachokera pa 1 Akorinto 7:29.
2. Kodi mungatani kuti muziyembekezera mwachidwi tsiku la msonkhano wapadera ukubwerawu?
2 Tsiku la msonkhano wapadera likangolengezedwa mumpingo mwanu, yambani kukambirana zosangalatsa zimene mukuyembekezera pamsonkhano umenewu. Makolo ena amathandiza ana awo kuyembekezera mwachidwi msonkhano mwa kulemba tsiku la msonkhanowo pa kalendala yawo. Iwo amalembanso zinthu zina zimene aliyense m’banjamo adzafunikire kutenga popita kumsonkhanoko. Kenako, amachotsera masikuwo mpaka tsiku la msonkhanowo litafika. Panthawi ya Kulambira kwa Pabanja, mwina mungakonde kukambirana mfundo zimene munalemba pa masiku a misonkhano yapadera ya m’mbuyomu. Mungathenso kukonzekeretsa mtima wanu mwa kuonanso mfundo za m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, patsamba 13 mpaka 16. Zimenezi zingathandize kuti inuyo ndi banja lanu ‘mudzasamale ndi kamvedwe kanu.’—Luka 8:18.
3. Kodi tingatani kuti tidzapindule kwambiri ndi zimene tidzaphunzire kumsonkhanowu?
3 Gwiritsani Ntchito Zimene Mwaphunzira: Nthawi zambiri msonkhano ukatha abale amakonda kunena kuti, “Koma msonkhanowu ndiye unali wosangalatsa bwanji!” Zoonadi, nthawi zonse misonkhano imakhala yosangalatsa popeza ndi chimodzi mwa zinthu zabwino zimene Yehova amapereka. (Miy. 10:22) Koma kuti zimene mwaphunzira zikhale zothandiza, muyenera kuzisinkhasinkha ndi kuzisunga m’maganizo mwanu. (Luka 8:15) Pobwerera kunyumba pambuyo pamsonkhanowu, mungachite bwino kumakambirana ndi banja lanu kapena anthu amene mukuyenda nawo mfundo zimene mwaphunzira. Kambiranani zolinga zimene aliyense ali nazo ndiponso mfundo zimene zingakuthandizeni mu utumiki wanu. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti mupindule ndi zimene mwaphunzira kumsonkhanowu ngakhale patapita nthawi yaitali.—Yak. 1:25.
4. N’chifukwa chiyani msonkhanowu udzakhala wapadera kwa ife?
4 Nthawi zonse timasangalala kwambiri tikapatsidwa mphatso yogwirizana ndi zimene tikusowa. Kodi si zoona kuti nafenso tikuyembekezera mwachidwi zimene Yehova watikonzera patsiku la msonkhano wapadera ukubwerawu? Tikukhulupirira kuti msonkhano umenewu udzakhala wothandiza m’njira zambiri. Tikuyembekezera kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova, adzatipatsa mphatso yoyenera mwa kutilimbikitsa ndi kutiphunzitsa kuti tigwire ntchito imene watipatsa.—2 Tim. 4:2; Yak. 1:17.
[Mafunso]