“Kodi Ndingaipeze Kuti Nthaŵi?”
1 N’zimene ambirife timanena, popeza moyo wathu uli ndi zochita zambiri. Anthu amati pa zinthu zimene tili nazo, chinthu chofunika kwambiri komanso chosachedwa kutha ndicho nthaŵi. Chotero kodi tingaipeze kuti nthaŵi yochitira zinthu zofunika kwambiri, monga kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu?—Afil. 1:10.
2 Chinsinsi chake ndicho kusankha zimene tikufuna kuchita pa nthaŵi imene tili nayo osati kufunafuna nthaŵi yochuluka. Tonse tili ndi maola 168 pamlungu, ndipo maola 100 pa maola ameneŵa tingawagwiritse ntchito pogona ndiponso pogwira ntchito. Choncho kodi maola otsalawo tingawagwiritse ntchito bwino motani? Aefeso 5:15-17, NW, amatilangiza kuti tiyende ‘osati ngati anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, ndipo tiwombole nthaŵi ndi kuzindikira nthaŵi zonse chifuniro cha Yehova.’ Izi zikusonyeza kuti tifunika kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuchita zinthu zimene Yehova akuti n’zofunika.
3 Yesu anayerekezera masiku athu ano ndi masiku a Nowa. (Luka 17:26, 27) Anthu nthaŵi imeneyo anatanganidwa ndi zochitika pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Komabe, Nowa anapeza nthaŵi yomanga chingalawa chachikulu ndiponso yolalikira. (Aheb. 11:7; 2 Pet. 2:5) Kodi nthaŵi anaipeza kuti? Mwa kuyamba kuchita zimene Mulungu amafuna komanso mwa kuzichita “momwemo.”—Gen. 6:22.
4 Kodi Patsogolo Pazikhala Chiyani? Yesu ananena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mat. 4:4) Mlungu uliwonse, timalandira ‘phoso [lauzimu] panthaŵi yake.’ (Luka 12:42) Phoso limeneli nthaŵi zonse limafunika kuliŵerenga ndi kuliphunzira patokha kuti timvetsetse zonse ndi kupindula nalo. Chifukwa chakuti timayamikira chakudya chauzimu, sitichiona monga chakudya chokonzedwa mwachangu, chofunika kuchidya mothamanga ngati momwe munthu angadyere chakudya mofulumira. Komano, kuyamikira kumatilimbikitsa kupeza nthaŵi yophunzira ndi kusangalala ndi zinthu zauzimu.
5 Kudya chakudya chauzimu kungatitsogolere ku moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kudya chakudya chauzimu n’kofunika kukhala patsogolo pazinthu zimene timachita tsiku lililonse. Kodi tingaipeze nthaŵi yoŵerenga Baibulo tsiku lililonse komanso yokonzekera misonkhano yachikristu? Inde, tingaipeze. Mwa kutero, tidzalandira “mphotho yaikulu” imene imadza chifukwa chodziŵa ndi kuchita zimene Mulungu amafuna.—Sal. 19:7-11.