Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov. 15
“Tamvapo mawu akuti, ‘Yesu amapulumutsa’ kapena akuti ‘Yesu anatifera.’ [Nenani mawu a pa Yohane 3:16.] Kodi munadzifunsapo momwe imfa ya munthu mmodzi ingapulumutsire tonsefe? [Muyembekezeni ayankhe.] Baibulo limayankha mosavuta. Mutu uwu wakuti, ‘Kodi Yesu Amapulumutsa Motani?,’ ukufotokoza bwino nkhani imeneyi.”
Galamukani! Dec. 8
“Kodi anthu akuchita zonse zimene angathe poteteza chilengedwe? [Muyembekezeni ayankhe.] Anthu ambiri amafunsa ngati zamoyo zonse padziko lapansili zidzakhale ndi moyo kosatha. Ubwino wake, zimenezi n’zomwe Mulungu akufuna. [Ŵerengani Nehemiya 9:6.] Galamukani! imakamba za momwe moyo padziko lapansi udzakhalire m’tsogolomu.”
Nsanja ya Olonda Dec. 1
“Nyengo ino, anthu ambiri amatanganidwa kwambiri kupereka mphatso ndi kuchita zinthu zina n’zina zachifundo. Zimenezi zimatikumbutsa Lamulo la Chikhalidwe. [Ŵerengani Mateyu 7:12.] Kodi mukuganiza kuti zingatheke kutsatira lamulo limeneli nthaŵi zonse? [Muyembekezeni ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo zambiri zofunika kuzilingalira pankhani yakuti ‘Lamulo la Chikhalidwe—Kodi Likugwirabe Ntchito?’”
Galamukani! Dec. 8
“Baibulo limalonjeza kuti tsiku lina palibe adzanene kuti, ‘Ndikudwala.’ [Ŵerengani Yesaya 33:24.] Mogwirizana ndi lonjezo limeneli, Galamukani! iyi ikukamba za matenda amene amagwira anthu ambiri, ana ndi akulu omwe. Lili ndi mutu wakuti ‘Odwala Nyamakazi Asataye Mtima.’ Ndikukhulupirira kuti muphunzira kenakake m’nkhani zimenezi.”