Madalitso Amene Amabwera Chifukwa Choyamikira Chikondi cha Yehova—Gawo 2
1 Mwezi watha pa gawo la nkhani iyi, tinatchula njira zinayi zomwe tingasonyezere kuti timayamikira chikondi cha Yehova mu utumiki. (1 Yoh. 4:9-11) Pano tiwonjezera njira zina zisanu za mmene tingachitire zimenezi. Timapeza madalitso ngati tichita nawo mokwanira ntchito yothandiza anthu ena mwauzimu.
2 Ulaliki Wamwamwayi: Iyi ndi njira yabwino yopezera anthu a njala ndi a ludzu la chilungamo komanso yowapatsira mabuku othandiza. Ndibwino ‘kuwombola nthaŵi’ ndiponso kulalikira nthaŵi zonse kwa onse amene timakumana nawo. (Aef. 5:16, NW) Tingafunike kulimba mtima kuti tilalikire mwanjira imeneyi, koma ngati tizindikira chikondi cha Mulungu ndi zosoŵa za anthu, tidzalalikira pampata uliwonse.—2 Tim. 1:7, 8.
3 Mmishonale wina anadalitsidwa kwambiri chifukwa choyamba kulankhulana ndi mwamuna wina amene anakwera naye galimoto. Mwamunayo anasonyeza chidwi. Anakonza zodzakumananso, ndipo anayamba naye phunziro la Baibulo. Mwamuna uja analoŵa m’choonadi ndipo anapita patsogolo mpaka anakhala mkulu mu mpingo.
4 Kulemba Makalata: Mwina timalephera kupita kunyumba ndi nyumba chifukwa cha matenda ena. Tingalembe makalata, kulalikira mwachidule anthu amene timawadziŵa, amene okondedwa awo amwalira, kapena amene sitinawapeze panyumba m’gawolo. Tingaikemo limodzi la mathirakiti athu a panthaŵi yake limene lili ndi uthenga wa m’Baibulo wosangalatsa ndiponso limene limalimbikitsa amene walandirayo kuti alembe kalata ngati ali ndi funso lililonse. Gwiritsani ntchito adiresi yanu kapena ya Nyumba ya Ufumu; chonde musagwiritse ntchito adiresi ya ofesi ya nthambi.
5 Ulaliki wa Patelefoni: Iyi ndi njira yabwino yopezera anthu amene timalephera kukumana nawo pantchito ya kunyumba ndi nyumba. Tikachita mwanzeru, mokoma mtima, ndi mwaluso, tingapeze zotsatira zabwino kwambiri. Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2001, tsamba 4, ndime 5 ndi 6 umasonyeza madalitso a ntchito imeneyi.
6 Mlongo wina akulalikira patelefoni, anafunsa mayi wina ngati analingalirapo za tsogolo lake ndi la banja lake. Mayiyo anati analingalirapo. Ndipo anati anachoka kwawo chifukwa chosoŵa mtengo wogwira. Mayi uja ataona momwe nkhaniyo inakhudzira mlongoyo, anavomera kuti adzakumane pamsika wapafupi ndi kwawoko. Kenako, mayi uja anavomera kuphunzira Baibulo.
7 Kulandira Alendo: Ngati timakonda anansi athu, tidzakhala tcheru kuona munthu wachilendo aliyense amene wabwera pa malo athu osonkhanira ndipo tidzam’thandiza kukhala womasuka. (Aroma 15:7) Tim’thandize kuona kuti ali pakati pa anthu amene akumufunira zabwino mwauzimu. Chikondi chathu chenicheni ndi kumuuza kuti tiziphunzira naye Baibulo zingam’limbikitse kulandira thandizo lathu.
8 Khalidwe Lathu Labwino: Mwa khalidwe lathu labwino, timakometsera choonadi. (Tito 2:10) Anthu a m’dziko akamanena zabwino za ife monga Mboni za Yehova, amalemekeza Mulungu wathu. (1 Pet. 2:12) Izinso zingathandize ena kuyamba kuyenda panjira ya ku moyo.
9 Bwanji osaona njira zisanuzi za mmene tingasonyezere kuyamikira kwathu chikondi chachikulu cha Yehova pa ife ndi kuzigwiritsa ntchito? (1 Yoh. 4:16) Mukatero, mudzapeza madalitso ochuluka kwambiri.