Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/02 tsamba 4
  • Pitirizani Kupindula ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kupindula ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 4/02 tsamba 4

Pitirizani Kupindula ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Popeza kuti tsopano tikusiya kutumiza papositi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa amene analembetsa, m’pofunika kuyesetsa kuti amene timawalalikira azilandira magazini onse.

Magazini Anuanu: Sabusikiripishoni yanu ikatha, kawonjezeni oda ya magazini anu kwa wamagazini. Makolo aziitanitsa magazini okwanira kuti aliyense m’banjamo azikhala ndi magazini yakeyake. Kulemba dzina pa magazini yanu kudzakuthandizani kusagaŵira magaziniyo mwangozi mu utumiki. Magazini akabwera, abale amene amayang’anira zimenezi azimasula mwamsanga magaziniwo ku Nyumba ya Ufumu.

Anthu Amene Timawagaŵira Magazini: Pali anthu achidwi amene amafuna kuti azilandira magazini mwezi ndi mwezi. Choncho ofalitsa azikhala ndi mayina a anthuwo oti magazini atsopano akabwera azikawagaŵira. Akamapereka magazini pamanja kwa anthu amenewo, zimathandiza kukulitsa chidwi chawo ndiponso kuyamba nawo phunziro la Baibulo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1998, tsamba 8.

Anthu a Zosoŵa Zapadera: Ngati munthu wasonyeza chidwi ndi mtima wonse koma amakhala m’gawo limene kulibe mpingo, angaloledwe kulembetsa magazini kuti aziwalandira papositi. Ngati sizitheka kumakam’patsa magazini munthu wa m’gawo la mpingo wanu koma akufunitsitsa kuti azilandira magazini, kambiranani ndi Komiti ya Utumiki ya Mpingo. Akavomereza, mungalembe mafomu olembetsera magazini. Gwiritsani ntchito mafomu a (M-1 ndi M-101).

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kudalitsa ntchito yathu yonse yolengeza Ufumu pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena