Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/02 tsamba 5-6
  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 4/02 tsamba 5-6

Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 7 kufikira April 22, 2002. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Zonama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Mfundo yomwe Solomo akutchula pa Mlaliki 2:2, ndi yakuti anthu sayenera kuseka ndiponso sayenera kukhala achimwemwe. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 9/15 tsa. 24 ndime 5.]

2. Yesaya 38:5 amatithandiza kuzindikira kuti mapembedzero oona mtima angapangitse Yehova kuchita chinthu chimene sakanachita. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95 4/1 tsa. 15.]

3. Pa Yesaya 1:7, mneneriyu akunena za kuwonongedwa kwa Yuda mu ulamuliro wa Ahazi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 17 ndime 16.]

4. ‘Kuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa’ kotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9, kumasonyeza kuti kukachitika kumwamba. [rs-CN tsa. 209 ndime 4]

5. ‘Kulemekeza Yehova’ mooloŵa manja ndi zinthu zathu—nthaŵi yathu, luso lathu, nyonga zathu, ndi chuma chathu kumadzetsa madalitso ochuluka ochokera kwa Yehova. (Miy. 3:9, 10) [w00-CN 1/15 tsa. 25 ndime 1]

6. Koresi anakhala “wodzozedwa” wa Yehova ngakhale kuti palibe umboni wosonyeza kuti anam’tsanulira mafuta enieni. (Yes. 45:1) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 11/15 tsa. 30.]

7. Malinga ndi zomwe Mateyu 24:38, 39 amasonyeza, kudya ndi kumwa, limodzi ndi ntchito zina za anthu, zinachititsa anthu a m’tsiku la Nowa kupululuka ndi Chigumula. [w00-CN 2/15 tsa. 6 ndime 6]

8. Nthaŵi zonse, Yehova amapereka zimene atumiki ake odzichepetsa amene amam’tumikira mopanda dyera am’pempha. [w00-CN 3/1 tsa. 4 ndime 3]

9. “Amitundu” otchulidwa pa Yesaya 60:3 ndi magulu andale osiyanasiyana omwe akopeka ndi kuwala koperekedwa ndi Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w00-CN 1/1 tsa. 12 ndime 4.]

10. Yehova ‘anapatula’ Yeremiya asanabadwe chifukwa chakuti Iye anakonzeratu zomwe zidzachitikire Yeremiya m’tsogolo. (Yer. 1:5) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 4/1 tsa. 10 ndime 2.]

Yankhani mafunso otsatiraŵa:

11. Pa Mlaliki 11:1, kodi ‘kuponya zakudya’ kumatanthauzanji? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 9/15 tsa. 25 ndime 11.]

12. Pa Yesaya 6:8, kodi Yehova akuphatikiza ndani pamene akunena kuti “ife”? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN mas. 94-95 ndime 13.]

13. Pa kukwaniritsidwa kwa Yesaya 9:2, kodi “kuŵala kwakukulu” kunaunika motani m’Galileya? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 126 ndime 17.]

14. Kodi kugwa kwa Babulo mu 539 B.C.E. ndi kufafanizidwiratu pambuyo pake, kukufanana ndi zochitika ziti zamakono? (Yes. 13:19, 20; 14:22, 23) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 188 ndime 30-1.]

15. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala motani monga “mlonda” wofotokozedwa pa Yesaya 21:6? (Mat. 24:45) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN mas. 221-2 ndime 11.]

16. Kodi pa Miyambo 31:10 pali malangizo abwino otani opita kwa mnyamata amene akufuna mkazi woti akwatire? [w00-CN 2/1 tsa. 31 ndime 1]

17. Pa Yesaya 43:9 kodi milungu yomwe anthu amailambira ikutokosedwa motani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 2/1 tsa. 16 ndime 3.]

18. Kodi mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi ‘okongola’ motani? (Yes. 52:7) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 4/15 tsa. 27 ndime 6.]

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisanyengedwe ndi mtima wathu? (Yer. 17:9) [w00-CN 3/1 tsa. 30 ndime 4]

20. Kodi anthu ‘oyenda m’njira ya Yehova’ ayenera kuchitanji? (Yer. 7:23) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 8/15 tsa. 29 ndime 6.]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. “Wanzeru, mtima wake uli ku dzanja lake lamanja” mlingaliro lakuti ‘dzanja lamanja’ kaŵirikaŵiri limasonyeza ․․․․․․․․ motero, zimenezi zikusonyeza kuti ․․․․․․․․ wake umam’limbikitsa kuyenda m’njira yabwino, m’njira yoyanjidwa. (Mlal. 10:2; Mat. 25:33) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 9/15 tsa. 25 ndime 8.]

22. Lerolino, ‘ntchito yachilendo’ yoloseredwa pa Yesaya 28:21 ndiyo kuwonongedwa kwa ․․․․․․․․ , omwe amati ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 295 ndime 16; tsa. 301 ndime 28.]

23. Yemwe adzasakaze mizinda ya Yuda, amene wafotokozedwa pa Yesaya 33:1, ndi ․․․․․․․․ , ndipo iyenso adzagonjetsedwa, mu 632 B.C.E., nadzasiyira anthu okhala mu ․․․․․․․․ zofunkha, zomwe iwo ‘adzazisonkhanitse monga ziwala zisonkhana.’ (Yes. 33:4) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 343 ndime 4; tsa. 345 ndime 6.]

24. Kufananitsa Yesaya 54:1 ndi Agalatiya 4:26, 27 kumasonyeza kuti “[mkazi, NW] wouma” amaimira “ ․․․․․․․․ ndipo “mkazi wokwatibwa,” amaimira ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 8/1 tsa. 11 ndime 8.]

25. Tikanyozedwa ndiponso kukanidwa mu utumiki wathu, tiyenera kukumbukira kuti chitsutso choterocho sakuchitira ․․․․․․․․ , koma ․․․․․․․․ , Mwini uthenga wathu. (2 Akor. 4:1, 7) [w00-CN 1/15, tsa. 21 ndime 2]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Polemba masomphenya aulemerero wakumwamba wa Yesu, Paulo anadzitcha “mtayo,” kutanthauza kuti (iye anali atangobadwa kumene mwauzimu; anali woyambirira kulandira ntchito yokhala mtumwi kwa amitundu; kunali ngati kuti wapatsidwa ulemu wobadwa, kapena kuukitsidwa, ku moyo wauzimu nthaŵi yake isanakwane). (1 Akor. 9:1; 15:8) [w00-CN 1/15 tsa. 29 ndime 6]

27. Dzina lakuti “Atate Wosatha” limanena za mphamvu ndi udindo wa Mfumu yaumesiya wopatsa anthu (nyonga yauzimu; moyo wosafa kumwamba; chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi). (Yes. 9:6; Yoh. 11:25, 26) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN tsa. 131 ndime 26.]

28. M’kukwaniritsidwa kwamakono kwa Yesaya 66:7, “mwana wamwamuna” yemwe anabadwa amaimira (Yesu Kristu; Ufumu waumesiya; mtundu watsopano wauzimu m’chaka cha 1919). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 1/1 tsa. 11 ndime 3.]

29. Kuŵerenga mosamala kwambiri lemba la Mateyu 10:28 kumatithandiza kuona kuti Gehena wa moto (ndi malo ozunzirako munthu wamoyo; amaimira kuwonongedweratu; amasonyeza chidani cha Mulungu). [rs-CN tsa. 149 ndime 1]

30. M’kukwaniritsidwa kwamakono, “mtundu wosamvera mawu a Yehova,” wotchulidwa pa Yeremiya 7:28, umaimira (Babulo Wamkulu; Matchalitchi Achikristu; ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 4/1 tsa. 18 ndime 10.]

Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zomwe zili m’munsizi:

Miy. 24:16; Mlal. 3:11; Yes. 40:8; Mlal. 7:21, 22; 1 Pet. 4:6

31. M’nthaŵi yake yoyenera, cholinga cha ntchito iliyonse ya Mulungu chidzavumbulidwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 9/15 tsa. 24 ndime 8.]

32. Ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu akufa mwauzimu ikuwapatsa mwayi wolapa. [rs-CN tsa. 205 ndime 3]

33. Ngakhale kuti zinthu zododometsa pamoyo ndi zosapeŵeka, munthu wa Mulungu amayesetsabe kuchita chabwino. [w00-CN 2/1 tsa. 5 ndime 1]

34. Palibe chimene chingalepheretse kapena kuletsa kukwaniritsidwa kwa mawu a Mulungu, kapena chifuno chake chonenedwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani ip-1-CN mas. 401-2 ndime 10.]

35. Musadzinyenge mwa kuyembekezera kuchita zinthu zangwiro, kapenanso kuyembekezera kuti anthu opanda ungwiro adzachita zinthu zangwiro. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 3/1 tsa. 8.]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena