Valani ndi Kudzikongoletsa Bwino
1 Lipoti la m’nkhani ina linati: “Amuna onse, ndi ana omwe, avala mataye. Amayi ndi atsikana onse, ndiponso ang’onoang’ono, avala madiresi kapena masiketi. Palibe wovala jinzi kapena malaya opanda taye. Onse pano ndi ooneka bwino.” Kodi linali kunena za gulu liti? Anthu pa msonkhano wandale? Osonkhana pa maseŵero? Pa dansi? Ayi ndithu! limanena za gulu la abale ndi alongo pa msonkhano waukulu wachigawo.
2 Pa msonkhano wa mu mzinda wina, mtolankhani wa nyuzipepala ina ponena za khamu la Mboni, anati: “Amuna onse ndi ooneka bwino ndipo ovala masuti ndi mataye. Akazi ndi ovala zovala zopatsa ulemu komanso zokongola.” Mlonda wina mu mzinda womwewu amene anaona anthuŵa, ananenanso kuti: “Ndinu anthu akhalidwe, aulemu, aukhondo. Zimene ndikuona n’zokongola. M’dziko lauve lino, mwakwanitsa kuthetsa uve.” Inde, akutichitira umboni wabwino zedi! Kodi sitikusangalala kuti anthu akuyamikira kwambiri ubale wathu? N’zoona kuti Mboni zonse zinathandiza mwa kudzisamalira kuti pakhale malipoti abwino.
3 Timadziŵika padziko lonse chifukwa maonekedwe athu amasiyana kwambiri ndi a anthu ena. (Mal. 3:18) Chifukwa? Chifukwa chakuti timatsatira malangizo a m’Malemba akuti ‘tidziveke tokha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; . . . umo mokomera [amene] amavomereza kulemekeza Mulungu.’—1 Tim. 2:9, 10.
4 Kodi Zovala Zanu ndi Kudzikongoletsa Kwanu Kumasonyezanji? Zovala zathu ndiponso mmene timavalira zimanena za ife—zikhulupiriro zathu, mtima wathu, ndiponso zolinga zathu. Masitayelo amene timasankha amanena kuti ndife ndani ndiponso kuti timaimira chiyani. Tisalimbikitse maganizo ndi khalidwe loipa lotchuka m’dzikoli. Tisadere nkhaŵa kuti kaya sitayeloyi ndi yotchuka kwambiri kapena ayi koma tidere nkhaŵa kuti kodi ndi yoyenera kwa amene amati ndi mtumiki wa Mulungu? (Aroma 12:2) M’malo mofuna kuoneka ngati munthu wopanduka kapena wachiwerewere, tikufuna kusonyeza kuti ‘timalemekezadi Mulungu.’—1 Pet. 2:12.
5 Nthaŵi zina, munthu watsopano, wosazoloŵera, kapena wofooka mwauzimu angatengeke ndi zovala ndiponso kudzikongoletsa kulikonse kotchuka m’dzikoli popanda kuona kuti zikupereka malingaliro otani ponena za Yehova ndi gulu lake. Tonsefe tidzipende kuti tione ngati tatengera maganizo a dzikoli. Tingafunse mbale kapena mlongo amene amapatsidwa ulemu, wokhwima mwauzimu kuti atiuze moona mtima ponena za mavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu ndiyeno tilingalire mozama mfundo zimene atiuzezo.
6 Ena amavomereza kuti ndi zoona kuti afunika kuvala bwino pamsonkhano. Komano panthaŵi yocheza mapulogalamu a tsikulo akatha amavala motayirira. Khalanibe ndi miyezo yapamwamba yoyenera atumiki achikristu. (2 Akor. 6:3, 4) Kulikonse kumene timakumana ndi anthu, mabaji athu amsonkhano komanso kuvala ndi kudzikongoletsa kwathu kwabwino zimasonyeza kuti ndife Mboni za Yehova. Choncho, nthaŵi zonse zovala zathu zizikhala zabwino ndi zopatsa ulemu, kusonyeza kuti ‘sitili a dziko lapansi.’—Yoh. 15:19.
7 Tiyeni pa Msonkhano Wachigawo wachaka chino wakuti “Olengeza Ufumu Achangu” tikachite zimene tingathe kuti titsimikizire kuti ndife “mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu [wathu].” Mbiri yabwino imene imatsatirapo idzathandiza kuti Yehova ‘alemekezeke, amveke dzina, ndipo [apatsidwe] ulemu.’—Deut. 26:19.
[Bokosi patsamba 6]
Momwe Tingalemekezere Yehova:
■ Valani moyenera atumiki a Mulungu.
■ Peŵani kutengera masitayelo a dziko.
■ Khalani ndi malire, sonyezani kudziletsa.