Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kum’dziŵa Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Simungakane kuti n’kovuta kukhulupirira munthu amene sitikum’dziŵa bwino, si choncho kodi? Komatu Baibulo limatilimbikitsa kufunafuna Mulungu. [Ŵerengani Machitidwe 17:27.] Nkhani izi zikusonyeza momwe tingam’dziŵire bwino Mulungu.”
Galamukani! June 8
“Olamulira a mayiko osiyanasiyana ayesa njira izi ndi izi kuti athetse mavuto athu. Njira ina yatsopano imene ayesa ndi ya kudalirana pa zinthu zosiyanasiyana. Mungaŵerenge m’magazini iyi momwe njira imeneyi ikukukhudzirani pakalipano. Mungaŵerengenso za njira imene Baibulo linaneneratu kuti ndi imene idzathetse mavuto padziko lonse.” Ndiyeno ŵerengani Mateyu 6:9, 10.
Nsanja ya Olonda June 1
“Chifukwa cha zimene zikuchitika masiku ano anthu akufunsa chifukwa chake anthu osalakwa amafa msanga. Kodi munalingalirapo chifukwa chake anthu amafa? [Yembekezani ayankhe, ndiyeno pitani pabokosi la patsamba 7.] Ndikhulupirira mungakonde kudziŵa zimene Baibulo limanena pa imodzi mwa mfundo zabodza izi zomwe n’zofala, si choncho kodi?” Ngati n’zotheka ŵerengani lemba limene aika pamenepo.
Galamukani! June 8
“Anthu ambiri amaganiza kuti chipembedzo ndi sayansi siziyendera limodzi. Ena afika poganiza kuti munthu wokonda za sayansi sangakhulupirire Mulungu. Kodi inu mumaganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikufotokoza bwino kwambiri nkhani imeneyi.”