Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda June15
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kukhala wachimwemwe ngakhale tikukumana ndi mavuto? [Yembekezani ayankhe.] Magazini ino ikutiuza kumene tingakapeze malangizo oti n’kutithandiza kuthana ndi mavuto athu. Komanso ikufotokoza mmene kukhala ndi chiyembekezo chodalirika kumatilimbikitsira.” Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.
Galamukani! June
“Kodi simungavomereze kuti masoka amene achitika posachedwapa asonyeza kuti kumvera machenjezo n’kofunika? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene anthu opulumuka mphepo ya mkuntho ya Katrina anaphunzira pa tsoka limeneli. Ikutchulanso za chenjezo limene tonsefe tifunikira kumvera masiku ano.” Sonyezani nkhani yomwe yayambira patsamba 14.
Nsanja ya Olonda July 1
“M’dziko lathu lodzaza ndi mavuto lino, anthu ambiri amafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani moyo uli wodzaza ndi mavuto chonchi? Ngati Mulungu aliko, n’chifukwa chiyani sakuchitapo kanthu kuthetsa kuvutikaku?’ Kodi munayamba mwafunsapo mafunso ngati amenewa? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikuyankha mafunso amenewa mwa kupereka mayankho omveka bwino a m’Baibulo.” Werengani 2 Timoteo 3:16.
Galamukani! July
“Masiku ano, mabanja ambiri ali pamavuto. Kodi mukuganiza kuti zingakhale zothandiza ngati mwamuna ndi mkazi wake atagwiritsa ntchito malangizo ouziridwa awa? [Werengani Aefeso 4:32. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikufotokoza za malangizo a m’Baibulo, amene akhala akugwira ntchito kwa zaka zambiri, omwe angatithandize kukhala ndi banja losangalala.”