Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda June 15
“Kodi mukuganiza kuti mavuto ngati aŵa adzathadi? [Ŵerengani mawu mu nkhani yoyambayo onena zimene lipoti lina linanena, ndiyeno yembekezani ayankhe.] Mawu ouziridwa a Mulungu akutitsimikizira kuti mavuto ameneŵa atha posachedwapa. [Ŵerengani Salmo 72:12-14.] Nsanja ya Olonda iyi ikulongosola momwe zimenezi zidzachitikire.”
Galamukani! July 8
“Kodi mukuganiza kuti zidzatheka kuti anthu onse padziko lapansi akhale pa ufulu weniweni? [Yembekezani ayankhe.] Taonani lonjezo labwino ili la Mulungu. [Ŵerengani Aroma 8:21.] Koma kuti zimenezi zichitike, ukapolo uyenera kutha kaye, sichoncho kodi? Galamukani! iyi ikusonyeza momwe zimenezi zidzachitikire.”
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthu mamiliyoni ambiri amagwiritsa ntchito mafano kapena zifanizo polambira, ndipo anthu ena mamiliyoni ambiri amaganiza kuti kuchita zimenezi n’kulakwa. Kodi munayamba mwalingalira zimene Mulungu amaganiza pankhaniyi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Yohane 4:24.] Nkhani izi zikusonyeza momwe kulambira mogwiritsa ntchito zifaniziro kunayambira ndiponso zimene Baibulo limanena pankhani yolambira mafano.”
Galamukani! July 8
“Baibulo linalosera kuti masiku otsiriza adzakhala ovuta kwambiri. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1, 3.] Kuchuluka kwa upandu padziko lonse ndi umboni wa zimenezi. Zinthu zikanaipa kwambiri pakanakhala kuti palibe apolisi. Galamukani! iyi ikufotokoza mavuto amene apolisi padziko lonse amakumana nawo.