Samalirani Chuma Chimene Timagwiritsa Ntchito mu Utumiki wa Mulungu
1 Mfumu Yosiya pokonzekera kukonzanso kachisi, anauza anthu ogwira ntchitoyo kuti: “Sanawaŵerengera ndalamazo zoperekedwa m’dzanja lawo, pakuti anachita mokhulupirika.” (2 Maf. 22:3-7) Momwe anthu ameneŵa anagwiritsira ntchito zinthu zimene anaikizidwa, kunasonyeza kuti ankasamalira zinthu zopatulika. Ifenso masiku ano potumikira uthenga wabwino wa Mulungu, tifunika kusonyeza kukhulupirika pogwiritsa ntchito zinthu zimene taikizidwa.
2 Mu Utumiki Wakumunda: Kuzindikira kuti uthenga wa m’mabuku athu ndi wofunika kwambiri ndiponso kuti pamafunika ndalama zambiri kuti awapange, kumatipangitsa kuwasamala kwambiri. Tisamagaŵe chisawawa mabuku athu kwa anthu amene sayamikira kwenikweni uthenga wa Baibulo. Ngati munthu wasonyeza chidwi pang’ono ndi uthenga wabwino, tingam’patse thirakiti osati mabuku.
3 Gaŵirani mabuku mosonyeza kuti mumazindikira kufunika kwake. Peŵani kusiya mabuku pamtetete, pomwe angauluzike n’kungoti balala. Peŵani kuwononga magazini, mwa kuŵerenga amene mwatsala nawo kunyumba musanakawonjezere ena. Ngati nthaŵi zonse mumatsala ndi magazini, chepetsani oda yanu.
4 Mabuku Anuanu: Tiziitanitsa mabuku okhawo amene timafunikadi. Makamaka tichepetse kuitanitsa mabaibulo a chikuto chofeŵa, mabaibulo a malifalensi, ndi mabuku ena, monga Concordance, Index, mavoliyumu a Insight, ndiponso buku la Proclaimers, zomwe ndi zinthu zimene zimafuna ndalama zambiri.
5 Kodi mumalemba dzina ndi adiresi yanu m’mabuku anu? Izi zimathandiza kuti lina likasoŵa musamaitanitse lina. Ngati mwataya buku la nyimbo, Baibulo kapena buku lophunzirira, mukhoza kukalipeza ku zinthu zotayika pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo amsonkhano.—Luka 15:8, 9.
6 Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito mwanzeru mabuku athu. Iyi ndi njira imene tingasonyezere kukhulupirika kwathu pogwiritsa ntchito zinthu za Ufumu zimene Yehova watiikiza.—Luka 16:10.