Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira September 9
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kambiranani nkhani yakuti “Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Ikuyenda Bwino.”
Mph. 15: “Kuthandiza Ena Kulemekeza Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ingakuloleni, tchulani mfundo yabwino imodzi kapena ziŵiri za m’buku la Kukambitsirana, tsamba 420-423.
Mph. 15: N’chifukwa Chiyani Alibe Chikhulupiriro? Kukambirana ndi omvetsera. Nthaŵi zambiri timakumana ndi anthu osakhulupirira kwenikweni. (2 Ates. 3:2) Kuti tikambirane nawo choonadi cha Yehova, tiyenera kupeza kaye chifukwa chake ali ndi maganizo ameneŵo ponena za Mulungu. Pendani mfundo zinayi zimene zingalepheretse anthu kukhala ndi chikhulupiriro, za m’buku la Kukambitsirana, tsamba 67 ndi 68. Pemphani omvetsera kunena zimene tinganene titapeza anthu a maganizo ameneŵa.
Nyimbo Na. 122 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Limbikitsani onse kupenda notsi zimene analemba ku msonkhano wadera wapitawo pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamaŵa.
Mph. 18: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhaniyi ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pendani mfundo zazikulu pa lipoti lampingo la chaka chautumiki cha 2002. Yamikirani zinthu zabwino zimene anthu onse anachita. Kambani kwambiri za mmene mpingo wachitira pankhani yopezeka pamisonkhano, maulendo obwereza ndi pantchito yochititsa maphunziro a Baibulo ndi upainiya wothandiza. Tchulani zina zimene zingawathandize kupita patsogolo m’mbali zimenezi. Nenani zolinga zimene angathe kukwaniritsa m’chaka chimene chikubwerachi.
Mph. 17: Mavuto Amene Kholo Lomwe Lili Lokha Limakumana Nawo. Mkulu afunse kholo limodzi kapena aŵiri amene ali okha (kapena amene mkazi kapena mwamuna wawo si Mboni) kuti aone zimene amachita kuti athane ndi mavuto a kuphunzitsa, kulanga, ndi kutsogolera ana awo mwauzimu. Kodi amatha bwanji kusamalira zinthu za pabanja ndiponso kumapezeka pa misonkhano yampingo ndiponso mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse? Gogomezerani malangizo a m’buku la Chimwemwe cha Banja, tsamba 104 mpaka 110. Monga anenera patsamba 113 mpaka 115, tchulani njira zimene ena angathandizire anthu ameneŵa.
Nyimbo Na. 149 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya September 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye akuti: “Sindili wokondwera ndi Mboni za Yehova.”—Onani buku la Kukambitsirana, patsamba 17-18.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Opani Mulungu, M’patseni Ulemerero.” (Chiv. 14:7) Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera, kupenda pulogalamu ya msonkhano wadera umene unachitika chaka chautumiki chapitachi. Pemphani mpingo kutchula mfundo zazikulu zimene anaphunzira ndiponso momwe iwo agwiritsira ntchito mfundozo pawokha kapena pabanja. (Mutha kuwapatsiratu anthu mbali zimenezi.) Kambani mbali za pulogalamu izi: (1)“Thandizani Atsopano Kukhala Oopa Mulungu.” Kodi tingawathandize bwanji anthu amene anabwera pa Chikumbutso kupita patsogolo ndi kukhala atumiki a Yehova achangu? (2) “Kuopa Yehova Kumatanthauza Kudana ndi Choipa.” (w87-CN 4/15 17-18) Kodi Miyambo 6:16-19 angatithandize bwanji kupeŵa zinthu zimene Yehova amadana nazo monga kunyada, kunama, kukondetsa chuma, kusangalala ndi zinthu zoipa komanso kugwiritsa ntchito intaneti molakwa? (3) “Yandikirani Kwambiri Anthu Amene Mumawakonda.” Timakonda Yehova, Yesu, a m’banja lathu ndi anthu ena a mumpingo. Kodi kuyandikana kwambiri ndi anthu ameneŵa kumatiteteza motani ku zochitika za dzikoli? (4) “Opani Yehova, Osati Anthu.” Kodi kuopa kukhumudwitsa Yehova kwakuthandizani motani kuthetsa mantha polalikira, kutsatirabe mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu pantchito kapena kusukulu, kapena kukana zonena za abwana anu zakuti muphonye misonkhano yampingo, yadera, ndi yachigawo? (5) “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu.” (Sal. 119:37; Aheb. 4:13) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kumwetsa moŵa, kuonera zolaula, kapena kuchita machimo ena obisika chifukwa choopa Mulungu? (6) “Yendanibe Moopa Yehova.” Kodi Yehova wakudalitsani motani chifukwa cholola mzimu wake kugwira ntchito kwambiri pa moyo wanu?—Sal. 31:19; 33:18; 34:9, 17; 145:19.
Nyimbo Na. 171 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 30
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mu utumiki wakumunda a September. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, mkulu asonyeze momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndipo mtumiki wotumikira asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya September 8. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse nenani mawu oyamba amene anagwiritsa ntchito kuti adzutse chidwi cha mwininyumba.
Mph. 15: Kodi N’chiyani Chimapangitsa Magazini Athu Kukhala Apadera Kwambiri? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Mu October tidzagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kambiranani zimene zimapangitsa magazini ameneŵa kukhala apadera: (1) Amakweza dzina la Yehova. (2) Amalimbikitsa kukhulupirira Yesu. (3) Amalengeza Ufumu wa Mulungu. (4) Amanena kuti Baibulo ndilo umboni weniweni wa nkhani zonse. (5) Amafotokoza kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo. (6) Amafotokoza tanthauzo lenileni la zimene zikuchitika masiku ano. (7) Amafotokoza momwe tingathetsere mavuto a masiku ano. (8) Amachititsa chidwi anthu osiyanasiyana. (9) Saloŵerera m’ndale. Sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule, chilichonse chisonyeze momwe tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi mwa mfundozi kuyambitsira makambirano.
Mph. 15: “Samalirani Chuma Chimene Timagwiritsa Ntchito mu Utumiki wa Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu. Phatikizaniponso ndemanga za zinthu zimene zimachitika pampingopo ndi zimene mpingo ungachite kuti uzigwiritsa ntchito mabuku athu mwanzeru. Limbikitsani onse kuti azioda mabuku okhawo amene amagwiritsa nchito. Kumbukirani kuti ndi mwayi wathu kupereka kangachepe kothandizira ntchito yapadziko lonse.
Nyimbo Na. 21 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Kuimira Choonadi ku Sukulu. Funsani wofalitsa wachinyamata mmodzi kapena aŵiri amene ayambanso sukulu ndiponso amene akudziŵa kufunika kosamala pocheza ndi anzawo akusukulu osakhulupirira. Kodi amakonzekera motani kuti athane ndi mavuto ndiponso zokopa za miyambo ya fuko, magule a kusukulu ndi misonkhano ikuluikulu, maseŵera ena, ndi makhalidwe oipa? Phatikizanipo njira zimene amakonzekera kuti akagwiritse ntchito polalikira kusukulu.
Mph. 20: “Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu.” Woyang’anira utumiki ndi mkulu wina akambirane mfundo zazikulu za m’nkhaniyi. Gogomezerani cholinga chathu chowonjezerera zimene timachita mu utumiki.
Nyimbo Na. 105 ndi pemphero lomaliza.