Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov. 15
“Anthu ena afunsa ngati matchalitchi ndi akachisi ali ofunika polambira Mulungu. Kodi mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi. [Ŵerengani Machitidwe 17:24.] Choncho, kodi malo olambiriramo ayenera kugwira ntchito yanji? Magazini iyi ikuyankha funso limeneli mogwiritsa ntchito Malemba.”
Galamukani! Nov. 8
“Kodi mumaganiza kuti mapemphero a atsogoleri achipembedzo kapena a munthu wina aliyense angabweretse mtendere padziko lonse? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limalonjeza kuti nthaŵi ina dziko lonse lidzakhala pamtendere. [Ŵerengani Yesaya 9:6, 7.] Kodi mwaona kuti wolamulira winawake wapadera ndiye adzabweretse mtendere padziko lapansili? Galamukani! iyi ikutchula wolamulira ameneyu ndiponso mmene adzabweretsere mtendere weniweni.”
Nsanja ya Olonda Dec. 1
“Masiku ano, pafupifupi aliyense amavutika kuti apeze zinthu zofunika pamoyo. Chimodzimodzinso matchalitchi, ndipo achita kunyanya kupemphetsa ndalama. Kodi zimenezi zimakuvutitsani maganizo? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani 1 Atesalonika 2:9.] Nsanja ya Olonda iyi ikulongosola zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.”
Galamukani! Nov. 8
“Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti ikudza nthaŵi imene padzakhala palibe munthu wonena kuti, ‘Ndikudwala.’ [Ŵerengani Yesaya 33:24.] Kodi sizidzakhala zosangalatsa zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Komabe, masiku ano anthu akuvutika ndi matenda ambiri, ndiponso mliri wa Edzi. Galamukani! iyi ikuyankha funso lakuti, Kodi Edzi idzathetsedwa?”