Lalikirani Uthenga wa Ufumu
1 “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” (Luka 4:43) Ndi mawu ameneŵa, Yesu anasonyeza kuti mfundo yaikulu ya utumiki wake inali Ufumu wa Mulungu. Uthenga umene timalalikira masiku ano wagonanso pa Ufumu, monga momwe Mateyu 24:14 analosera kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Kodi ndi mfundo ziti za choonadi cha Ufumu wa Mulungu zimene anthu afunika kumva?
2 Ufumu wa Mulungu tsopano ukulamulira kumwamba ndipo posachedwapa udzatenga malo a maulamuliro onse a anthu. Mdyerekezi anathamangitsidwa kale kumwamba, ndipo dziko loipa lino lili m’masiku ake otsiriza. (Chiv. 12:10, 12) Dziko la Satana lakale ndi loipali lidzatheratu, koma Ufumu wa Mulungu sudzagwedezeka. Udzakhala kosatha.—Dan. 2:44; Aheb. 12:28.
3 Ufumu udzachita zinthu zabwino zimene anthu onse okhulupirika amafuna. Udzachotsa mavuto amene amabwera chifukwa cha nkhondo, upandu, kuponderezana ndiponso umphaŵi. (Sal. 46:8, 9; 72:12-14) Anthu onse adzakhala ndi chakudya chambiri. (Sal. 72:16; Yes. 25:6) Matenda ndi kupunduka zidzakhala zinthu zakale. (Yes. 33:24; 35:5, 6) Pamene anthu azidzakhala angwiro, dziko lidzasintha kukhala paradaiso, ndipo anthu adzakhala pamodzi mogwirizana.—Yes. 11:6-9.
4 Timasonyeza kuti tikufuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu mwa zimene tikuchita panopo. Uthenga wa Ufumu uyenera kukhudza zochita zathu zonse, komanso zolinga zathu ndiponso zinthu zimene timaika patsogolo. Mwachitsanzo, ngakhale kuti tili ndi udindo wopezera banja lathu zinthu zofunika pamoyo, tisalole zinthu zimenezi kutsamwitsa zinthu za Ufumu. (Mat. 13:22; 1 Tim. 5:8) Koma tiyenera kumvera langizo la Yesu lakuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zinthu zofunika pamoyo] zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mat. 6:33.
5 Anthu akufunika kuti amve uthenga wa Ufumu ndi kuchitapo kanthu nthaŵi isanathe. Tiyenitu tiwathandize kuchita zimenezi mwa ‘kuwakopa ponena za Ufumu wa Mulungu.’—Mac. 19:8.