Kodi Choyamba N’chiyani M’moyo Wanu?
1 Magulu ambiri achipembedzo amalimbikira kuchita ntchito zothandiza anthu, monga kumanga sukulu kapena kuthandiza pa ntchito zachipatala. Koma Mboni za Yehova, ngakhale kuti sizinyalanyaza “kuchitira chokoma ndi kugawira ena,” zimaika poyamba ntchito yothandiza anthu mwauzimu.—Aheb. 13:16.
2 Chitsanzo cha M’zaka 100 Zoyambirira: Yesu ankachita zinthu zabwino zosiyanasiyana nthaŵi ya utumiki wake wa padziko lapansi pano, koma ntchito yake yaikulu inali yochitira umboni za choonadi. (Luka 4:43; Yoh. 18:37; Mac. 10:38) Iye analamulira otsatira ake kuti “mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa.” (Mat. 28:19, 20) Ndipo anasonyeza kuti anthu amene adzam’khulupirire iye adzaigwira kwambiri ntchito imene anaiyambitsayi kuposa mmene anaigwirira iyeyo. (Yoh. 14:12) Ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri kuposa zonse pa moyo wa Yesu chifukwa imathandiza anthu kuphunzira mmene angapezere chipulumutso.—Yoh. 17:3.
3 Mtumwi Paulo anaiona ntchito yake yolalikira ngati ‘chomukakamiza,’ chinthu chimene sakanatha kuchinyalanyaza. (1 Akor. 9:16, 17) Iye anali wokonzeka kudzimana, kulimbana ndi mayesero, komanso kukumana ndi mavuto ena alionse kuti akwanitse utumiki wake. (Mac. 20:22-24) Mtumwi Petro ndi Akristu anzake analinso ndi mtima womwewo. Ngakhale pamene ankamenyedwa ndi kuikidwa m’ndende, “sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”—Mac. 5:40-42.
4 Nanga ife bwanji? Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso yopanga ophunzira ili pamalo oyamba m’moyo wathu? Monga mmene anachitira Yesu, kodi timawamvera chisoni anthu amene ali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa”? (Mat. 9:36) Zinthu zimene zikuchitika masiku ano, komanso ulosi wa Baibulo, zikusonyezeratu kuti dziko loipa lino latsala pang’ono kutha! Ngati nthaŵi zonse tikumbukira kufunika kwa ntchito yolalikirayi, zidzatithandiza kupitirizabe kulalikira mwachangu.
5 Pendaninso Mmene Zinthu Zilili M’moyo Wanu: Popeza zinthu zimasintha m’moyo wa munthu, ndi bwino kuti nthaŵi ndi nthaŵi tiziona ngati pali zina zimene tingazisinthe n’cholinga choti tizitha kulalikira kwambiri. Mlongo wina anali mpainiya m’zaka za m’ma 1950, 1960, komanso m’ma 1970, kenako analeka kuchita upainiya chifukwa cha kudwaladwala. Ndiye patapita nthaŵi, thanzi lake linakhalanso bwino. Posachedwapa, atapendanso mmene zinthu zilili, anaona kuti akhoza kuyambiranso kuchita upainiya. Tangoganizirani chimwemwe chimene anali nacho pochita nawo Sukulu ya Utumiki Waupainiya ali ndi zaka 90! Nanga inu bwanji? Kodi mwatsala pang’ono kupuma pantchito kapena kumaliza sukulu? Kodi chifukwa cha kusintha kwa zinthu kumeneku mungathe kuchita upainiya?
6 Yesu poona kuti Malita “anatekeseka ndi kutumikira kwambiri” anamuthandiza mwachikondi kuti azindikire kuti angakhale ndi madalitso ambiri posachulukitsa zochita. (Luka 10:40-42) Kodi mungapunguleko zina ndi zina m’moyo wanu? Kodi n’zofunikiradi kuti nonse bambo ndi mayi muzigwira ntchito? Mutasinthapo zinthu zina, kodi banja lanu lingakwanitse kugwiritsa ntchito ndalama za munthu mmodzi yekha basi? Anthu ochuluka apindula kwambiri mwa kusintha zinthu zina n’kukhala ndi nthaŵi yambiri yochitira utumiki.
7 Tonsefe tiyeni titsatire chitsanzo chimene anatisiyira Yesu ndi atumwi ake! Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzadalitsa zoyesayesa zathu zonse zochokera pansi pa mtima zimene tikuchita n’cholinga choti tithe kukhala ndi nthaŵi yochuluka yochitira ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Luka 9:57-62.