Utumiki Wachikristu Ndiyo Ntchito Yathu Yaikulu
1 Tonsefe tili ndi ntchito zosiyanasiyana zimene timagwira. Ndi lamulo lochokera kwa Mulungu kupezera banja lathu zinthu zofunika kwambiri pamoyo. (1 Tim. 5:8) Komabe, ntchito imene timagwira pofuna kukwaniritsa lamulo la Mulungu limeneli, isatipangitse kunyalanyaza ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
2 Yesu anapereka chitsanzo choti titsatire ‘pofuna [choyamba, NW] Ufumu.’ (Mat. 6:33; 1 Pet. 2:21) Ngakhale kuti analibe zinthu zambiri, anatanganidwa kwambiri ndi kuchita zofuna za Atate ake. (Luka 4:43; 9:58; Yoh. 4:34) Analalikira mwachangu zedi pampata uliwonse. (Luka 23:43; 1 Tim. 6:13) Iye analimbitsa ophunzira ake kukhalanso achangu mu ntchito yotuta.—Mat. 9:37, 38.
3 Kutsanzira Yesu Masiku Ano: Tingatsanzire chitsanzo cha Yesu mwa kuyesetsa kukhala moyo wosafuna zambiri umene umaika maganizo pa utumiki wachikristu. Ngati tili ndi zinthu zofunika kwambiri pamoyo, tiyeni timvere langizo la Baibulo lakuti tisapitirize kufunafuna zinthu zambiri m’dzikoli. (Mat. 6:19, 20; 1 Tim. 6:8) Zingakhale bwino kwambiri kufuna kuwonjezera zimene timachita mu ntchito yolalikira. Tikapeza mavuto, tilimbikire monga anachitira Yesu, tisalole mavutowo kudodometsa ntchito yathu yaikulu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Luka 8:14; 9:59-62.
4 Ngakhale amene ali ndi maudindo ambiri amaona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri. Mbale wina amene ali ndi banja lalikulu, udindo waukulu kuntchito, ndiponso ndi mkulu mu mpingo wachikristu anati: “Ndimaona utumiki kukhala ntchito yanga yaikulu.” Mlongo wina amene ndi mpainiya anati: “Upainiya ndi ntchito yapamwamba kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse.”
5 Kaya zinthu zili bwanji kwa inu, tiyeni titsatire chitsanzo cha Yesu. Motani? Mwa kupanga utumiki wachikristu kukhala ntchito yathu yaikulu.