Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/03 tsamba 1
  • Yehova Ndiye Woyenera Kulemekezedwa Kwakukulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Ndiye Woyenera Kulemekezedwa Kwakukulu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Makhalidwe Amene Amatichititsa Kupezeka Pamisonkhano
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 3/03 tsamba 1

Yehova Ndiye Woyenera Kulemekezedwa Kwakukulu

Mgonero wa Ambuye Udzachitika pa April 16

1 Panopa maso ali pa kalendala kuyang’anira tsiku la April 16, 2003. Usiku umenewo tidzakumbukira imfa ya Yesu mogwirizana ndi olambira anzathu mamiliyoni padziko lonse kulemekeza dzina la Yehova. Yehova tiyenera kum’tamanda chifukwa cha mphatso yabwino ya dipo imene anatipatsa. Ndi mphatso imeneyi, iye adzadalitsa anthu onse omvera. Chotero tikugwirizana ndi wamasalmo ndi mtima wonse pofuula ndi mawu akuti: ‘Yehova ayenera kulemekezedwa kwakukulu.’—Sal. 145:3.

2 Nthaŵi imeneyi ndi yosinkhasinkha za ubwino wa Mulungu komanso za mangawa omwe tili nawo kwa Yehova omuyamikira potumiza “Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.” (1 Yoh. 4:9, 10) Tikasonyeza kumvera mwa kukumbukira Mgonero wa Ambuye, mitima yathu imakhudzika pozindikira kuti “Yehova ndiye wachisomo . . . ndi wa chifundo chachikulu.” (Sal. 145:8) Inde, dipo ndi umboni waukulu koposa wakuti Yehova amakonda anthu. (Yoh. 3:16) Tikaganizira za chikondi cha Mulungu komanso za kukhulupirika kwa Yesu, timalemekeza Yehova. Tidzam’lemekeza kosatha chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anaonetsa potipatsa mwayi wokhala ndi moyo wosatha.—Sal. 145:1, 2.

3 Thandizani Ena Kulemekeza Yehova: Kuyamikira kwathu dipo, mphatso yapamwamba ya imene Mulungu anapereka, kumatilimbikitsa kuitana ena kuti tilemekezere Yehova pamodzi. Wamasalmo anauziridwa kulemba kuti: “Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu.” (Sal. 145:7) Chaka chatha chokha, Mboni za Yehova padziko lonse zinathera maola oposa 1,000,000,000 pa ntchito yolalikira. Kodi khama lawolo linapindula chiyani? Kutengera avareji, anthu oposa 5,100 anabatizidwa pa mlungu uliwonse kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova. Pa anthu 15,597,746 amene anapezeka pa Chikumbutso, 9,000,000 sanayambe kutumikira Yehova monga ofalitsa a uthenga wabwino. Choncho, pali mpata woti tidzawonjezeka kwambiri! Monga olengeza Ufumu, timanyadira mwayi umene tili nawo wolalikira uthenga wabwino ndi kutsogolera mitima ya anthu ena kwa Yehova, Mwana wake, ndi Ufumuwo.

4 Njira yabwino yolimbikitsira ena kuti alemekeze Yehova ndiyo yowaitana kuti adzakhale nafe pa Mgonero wa Ambuye. Kodi mwalemba mayina a anthu amene mukufuna kudzawaitana kuphatikizapo aja amene munawauza kale koma adzangofunikira kuwakumbutsa za tsikulo ndi nthaŵi? Nanga kodi mwawaitana amene munaŵalemba mayinawo? Ngati simunachite zimenezi, yesetsani kutero nthaŵi yatsalayi. Athandizeni athu ameneŵa kuzindikira cholinga cha phwando limeneli. Pamwambowu, khalani maso ndipo perekani moni kwa alendo. Apangitseni kuona kuti mwawalandira, asonyezeni kwa ena kuti awadziŵe, ndipo ayamikireni chifukwa cha kupezekapo kwawo.

5 Kupezeka pa Chikumbutso kungalimbikitse atsopano kupita patsogolo mwauzimu. Munthu wina wophunzira Baibulo amene ali ndi vuto lokhala ndi mantha akakumbukira zoopsa zimene zinam’chitikira, ndipo amamangika akakhala pagulu, tsiku lina anafika pa Chikumbutso. Pamene anafunsidwa kuti afotokoze zimene anaona pamsonkhanowo, iye anati: “Usiku umene uja unali wopatulika, ndipo ndinali pomwepo.” Kuyambira pamenepo, anayamba kupezeka pa misonkhano.

6 Chikumbutso Chikadutsa: Kodi tingachite chiyani kuti tithandize anthu achidwi kuti afike potamanda Yehova? Akulu adziŵe atsopano amene afika pa Chikumbutso ndipo auze ofalitsa oyenerera kuwayendera anthu ameneŵa kuti akakambirane nawo zinthu zolimbikitsa zimene anaphunzira komanso zimene anaona pa Chikumbutsopo. Ena angafune phunziro la Baibulo la panyumba. Anthu ameneŵa aitanidwenso ku misonkhano ya mpingo yochitika mlungu uliwonse, chifukwa chakuti akamapezekapo nthaŵi zonse adzalidziŵa bwino kwambiri Baibulo.

7 Pali makonzedwe olimbikitsa onse amene ali osakhazikika ndi osagwira ntchito kuti azipezeka pamisonkhano mokhazikika. Chotero ngati mwapemphedwa ndi akulu kuti muthandize munthu wina amene wasiya kulalikira kuti ayambenso kuloŵa mu utumiki wa kumunda, khalani wofunitsitsa kuthandizapo. Kuonetsa chikondi choterocho kwa abale athu n’kogwirizana ndi mawu olimbikitsa a mtumwi Paulo amene anati: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.”—Agal. 6:10.

8 Tiyeni tonse tichite khama kuti tidzapezekepo pa Chikumbutso pa April 16. Sitikufuna kuti tidzaphonye mwambo wopatulika umenewu wotamanda Yehova. Inde, kuyambira panopa mpaka muyaya, tipitirizetu kuyamika Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu!—Sal. 145:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena