Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 10
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 15:“Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera.
Mph. 20: “Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!” (Ndime 1-12) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukakambirana ndime 6, khalani ndi chitsanzo chachidule. Wofalitsa akuitanira ku Chikumbutso wachibale, wachinansi, mnzake wa kusukulu, kapena wogwira naye ntchito, pogwiritsa ntchito kapepala koitanira anthu. Ngati ofalitsa sanalandirebe timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, muwagaŵire ukatha msonkhano.
Nyimbo Na. 19 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 17
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Sankhani Mwanzeru Ocheza Nawo. Ikambidwe ndi mkulu ndipo agwiritse ntchito Galamukani! ya March 8, 1997, patsamba 24, ndiponso mfundo zopezeka pa kamutu kakuti “Mayanjano Oipa,” tsamba 172 m’buku la Kukambitsirana. Sonyezani mmene mfundozo zikugwirira ntchito kwa achinyamata ndi achikulire omwe. Tsindikani phindu losankha mabwenzi amene amakonda Yehova ndiponso amene amasonyeza kuti akuyesetsa kutsatira malamulo ake.
Mph. 20: “Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!” (Ndime 13-26) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira wotsogolera. Pokambirana ndime 14, mkulu asonyeze chitsanzo chachidule cha ulendo wolimbikitsa mbale wokalamba wa thanzi lofooka. Afotokoze mokoma mtima mmene mbaleyo angachitire nawo ntchito yaikulu imeneyi ya mpingo panyengo ya Chikumbutso.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 24
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya March 15 ndi Galamukani! ya April 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsira ntchito magazini imodzi pokambirana.
Mph. 15 : Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20 : Mboni za Yehova Zimathandiza Anthu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Nthaŵi zina timakhala ndi mpata wofotokoza mmene utumiki wathu ndi chitsanzo chathu zimathandizira anthu. Pemphani omvetsera kuti anene ndemanga zawo pa mfundo zotsatirazi: (1) Timaphunzitsa anthu kuti azitsata mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo. (2) Timaphunzitsa anthu kukhala okhulupirika ndi kulemekeza olamulira. (3) Timaphunzitsa kuti mafuko, mayiko, ndi anthu osiyana chikhalidwe azigwirizana. (4) Timathandiza ena kuti mabanja awo azikhala abwino powalimbikitsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. (5) Taphunzitsa anthu ambiri kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba. (6) Timayesetsa kuthandiza ena nthaŵi za masoka a chilengedwe. (7) Takhala patsogolo kumenyera nkhondo ufulu wachipembedzo umene umapindulitsa onse. (Onani buku la Kukambitsirana, masamba 278, 279.) Kambiranani masiku a msonkhano wachigawo wa chaka chino ndi malo ake. Limbikitsani ofalitsa kuyamba kukonzekera zodzapezekapo masiku onse atatu.
Nyimbo Na. 121 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 31
Mph. 12 : Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa March. Tchulani mabuku ogaŵira mu April, makamaka tsindikani kuti tikufunika kuchita khama kwambiri kuti tiyambitse maphunziro a Baibulo mu buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. Kambiranani mfundo zazikulu pa “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.” Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za pa tsamba 6, sonyezani mmene mungagaŵire Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April 8.
Mph. 13: Zokumana nazo. Pemphani mpingo kuti ufotokoze zokumana nazo zimene zinawasangalatsa panthaŵi imene mpingo unali ndi ntchito yambiri mu March. Ayamikireni chifukwa cha khama lawo, ndiponso limbikitsani onse kuchita nawo ulaliki momwe angathere mu April.
Mph. 20: “Yehova Ndiye Woyenera Kulemekezedwa Kwakukulu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tsindikani kufunika kwa Chikumbutso. Sonyezani mmene onse angathandizire kuti ena akapezekepo. Fotokozani zimene tingachite kuti tithandize osagwira ntchito kuti akhalenso ndi chidwi. Funsani ofalitsa kuti afotokoze zokumana nazo zolimbikitsa za pa Chikumbutso cha chaka chatha.
Nyimbo Na. 173 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Mmene Mungakambirane ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Malemba. Kukambirana ndi omvetsera. Kodi tingakulitse bwanji luso lokambirana mogwira mtima ndi anthu mu utumiki? (1) Dziŵani bwino Malemba pochita phunziro laumwini nthaŵi zonse ndiponso popezeka pa misonkhano. (2) Muzisinkhasinkha zimene mumaphunzira, n’kupenda mfundo za choonadi zimenezo kuona kuti ndi nkhaninso ziti zimene zikukhudzidwa ndi mfundozo. (3) Musangomvetsa mmene afotokozera malembawo komanso mvetsani zifukwa za m’Malemba zimene afotokozera zimenezo. (4) Ganizirani mmene mungafotokozere malemba kwa anthu osiyanasiyana. (5) Ganizirani mmene mungachitire chitsanzo mfundo zina.
Mph. 20: Kukonzekera Nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Pendani mfundo zimene zili m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2002. Fotokozani bwino mmene ana a sukulu angakonzekere nkhani zawo.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 43-49.
Nyimbo Na. 217 ndi pemphero lomaliza.