Tsiku la Yehova Lili Pafupi
1 Akristu amalakalaka ndi mtima wonse tsiku la Yehova litabwera, pamene Yehova adzawononga dongosolo la zinthu lilipoli ndi kubweretsa dziko latsopano lachilungamo. (2 Pet. 3:12, 13) Popeza sitikudziwa nthawi yeniyeni imene tsikuli lidzafike, tifunika kukhalabe atcheru ndi kuthandizanso ena kuchita chimodzimodzi. (Ezek. 33:7-9; Mat. 24:42-44) Ngati tisinkhasinkha Mawu aulosi a Mulungu chikhulupiriro chathu chakuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi” chidzalimba.—Zef. 1:14.
2 Kutsatizana kwa Maulamuliro Amphamvu Padziko Lonse: Pa Chivumbulutso 17:9-11, mtumwi Yohane anatchula za “mafumu asanu ndi awiri,” kuimira maulamuliro asanu ndi awiri amphamvu padziko lonse otsatizana. Yohane ananenanso za ‘ufumu wachisanu ndi chitatu,’ umene panopa umaimira United Nations. Kodi tikuyembekeza kuti kudzabweranso maulamuliro ena amphamvu padziko lonse? Ayi, ulosiwo umanena kuti mfumu yachisanu ndi chitatuyo ‘inamuka kuchitayiko’ ndipo utadutsa ufumu umenewu sipakutchulidwanso maufumu ena padziko lapansi. Kodi ulosi umenewu ukukuthandizani kuona pamene tili m’nthawi imene tikukhalamo ino?
3 Lemba la Danieli 2:31-45 limatithandiza kumvetsa za kufika kwa tsiku la Yehova. Mu ulosiwo, fano lalikulu limene Nebukadinezara analiona m’maloto limaimira maulamuliro amphamvu padziko lonse otsatizana. Pa maulamuliro onsewo, uliwonse wakhalapo kale. Kodi ifeyo masiku ano, tafika pati m’mbiri ya anthu? Tili m’nthawi imene ikuimiridwa ndi mapazi a fanolo. Ulosiwo umafotokoza momveka bwino zimene zidzachitika pambuyo pake. Ulamuliro wa anthu udzawonongedwa kotheratu, kupereka mpata ku “ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse.” Kodi mukuona mmene zimenezi zikusonyezera kuti tsiku la Yehova lili pafupi?
4 Umboni Winanso: Lero tikuona ndi maso athu umboni winanso wosonyeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi. Tikuona kukwaniritsidwa kwa zimene mtumwi Paulo analosera zokhudza makhalidwe amene anthu adzakhala nawo ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1-5) Ndipo tikupereka nawo umboni padziko lonse umene uyenera kuperekedwa mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Ntchito yathu yolalikira ipitirize kusonyeza kuti uthenga wa mngelo wakuti, “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake” ndi uthenga wofunika kuchitapo kanthu mwamsanga.—Chiv. 14:6, 7.