Mphamvu Zazikulu za Dziko za Mbiri ya Baibulo Zipita ku Mapeto Awo!
KODI mungalingalire mbiri yakale yolembedwa pasadakhale? ‘Nchosatheka,’ mukutero? Komabe, pali bukhu limene ndithudi linanena mbiri pasadakhale—mazana, nthaŵi zina ngakhale zikwi za zaka zochitikazo zisanachitike! Bukhu limenelo ndi Baibulo.
Baibulo silimasimba kokha zochitika zakale ndi kulongosoka koma m’njira yozizwitsa kwambiri ilo linaneneratu ndandanda yaikulu ya mbiri ya dziko monga mmene ikayambukirira anthu a Mulungu, kuyambira nthaŵi ya Babulo wakale, zaka zoposa 2,500 zapita, kufikira ndipo ngakhale kupyola tsiku lathu.
Danieli, mneneri yemwe anakhalako m’zana lachisanu ndi chimodzi isanafike Nyengo Yathu, anapatsidwa zivumbulutso zinayi zosiyana zomwe zinachita ndi mtsogolo mwa mbiri ya dziko. Ndi kuti kumene iye anapeza chidziŵitso chake? Danieli ananena kuti: “Kuli Mulungu kumwamba Wakuvumbulutsa zinsinsi.” (Danieli 2:28) Akatswiri odziŵa za zinthu zofotseredwa pansi, akumafukula zotsalira zotsala mu mphamvu za dziko zakale, apeza chitsimikiziro chozizwitsa cha kuwona kwa ponse paŵiri mbiri ndi ulosi wopezeka m’Baibulo.
Ziŵiri za mphamvu zazikulu za dziko za m’mbiri ya Baibulo, Igupto ndi Asuri, zinakhalapo kwa nthaŵi yaitali nthaŵi ya Danieli isanafike. Babulo anali kulamulira m’tsiku la Danieli, ndipo maina a mphamvu za dziko ziŵiri zotsatira anavumbulidwa kwa mneneriyo. (Danieli 2:47, 48; 8:20, 21) Aŵiri ena akatsatira izi, kutibweretsa ife ku nthaŵi imene tiri.
Ndi zingati?
Mogwirizana ndi Baibulo, ndi zingati za mphamvu za dziko zoterozo zimene zikakhalapo? Yankho linaperekedwa kwa mtumwi wachikulire Yohane ndipo limasonyeza kumene tiri m’nyengo ya nthaŵi. Mngelo anauza Yohane kuti: “Ali mafumu asanu ndi aŵiri; asanu adagwa, imodzi iriko, inayo sinadze.”—Chivumbulutso 17:10.
Kodi ndi mphamvu za dziko zisanu ziti zomwe zinadza ndi kupita pofika m’tsiku la Yohane? Igupto, Asuri, Babulo, Medi-Peresiya, ndi Grisi. Ndi uti umene unali udakalipo? Roma. Ndipo ndi mphamvu iti imene “siinadze”? Mphamvu ya dziko ya Anglo-American ya tsiku lathu. Izi ndi mphamvu za dziko zimene anthu a Mulungu, akale ndi amakono, akhala akudera nazo nkhaŵa kwenikweni.
Nsonga yofunika kwambiri iri iyi: Kunafunikira kutsatizana kwa kokha zisanu ndi ziŵiri za mphamvu za dziko zoterozo! Mphamvu yachisanu ndi chitatu yowoneka pa nthaŵi imodzimodziyo, yomwe ikaphatikizapo yotsalira yachisanu ndi chiŵiri, inanenedweratu kukhalapo pa kanthaŵi kochepa mkati mwa masiku a yachisanu ndi chiŵiri. (Chivumbulutso 17:10, 11) Ichi chimatanthauza kuti tikukhala mkati mwa nthaŵi ya mphamvu yaikulu ya dziko yomalizira yolamuliridwa ndi munthu. Sipadzakhala ina yowonjezereka!
Mwamsanga tsopano, mphamvu za dziko zidzakhala ndi tsiku lawo. Danieli analosera kuti madongosolo a kachitidwe ka zinthu a anthu amenewa adzaphwanyidwa ndi ‘kutengedwa ndi mphepo.’ (Danieli 2:35) Nchiyani chimene chidzawalowa m’malo? Chinachake chabwino koposa! Danieli akusimba kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire,” kosatha. (Danieli 2:44) Chotero palibe china chirichonse chochepera kuposa Ufumu wa Mulungu womwe udzaloŵa m’malo mphamvu za dziko za anthu zimenezi. Kudzakhala kuwongokera kwakukulu kotani nanga mu ulamuliro wadziko!
Mosakaikira inu mukudziŵa chinachake ponena za mphamvu za dziko. Koma kodi chidziŵitso chowonjezereka cha miyambo yawo, zipembedzo zawo, ndi maunansi awo ndi anthu a Mulungu ndi ulosi wa Baibulo kumakuthandizani inu kumvetsetsa mowonjezereka ponena za mbiri ya mtundu wa anthu m’chiwunikiro cha Malemba?
Inde, ndithudi. Chotero tiri osangalatsidwa kufalitsa, kuyambira ndi kope lino, mpambo wa nkhani zisanu ndi zitatu zochita ndi mphamvu za dziko. Nkhani zimenezi ziyenera kuthandiza kukutsimikizirani kuti mbiri yonenedwa m’Baibulo iri yodalirika ndi yokhulupirika. Izo ziyenera kulimbikitsa chikhulupiriro chanu m’nsonga yakuti maulosi a Baibulo ali okhulupirika ndi owona!