Ndandanda ya Banja Yolowera mu Utumiki wa Kumunda
1 Yehova amasangalala akamaona achinyamata akulemekeza dzina lake. (Sal. 148:12, 13) M’nthawi ya Yesu ngakhale ‘makanda ndi oyamwa anafotokoza zolemekeza’ Mulungu. (Mat. 21:15, 16) Zofanana ndi zimenezi zikuchitikanso masiku ano. Makolo, kodi mungatani kuti muthandize ana anu kukhala achangu polemekeza Yehova mu utumiki wachikristu? Malinga ndi zimene yafotokoza nkhani ili pamwambayi yonena za misonkhano ya mpingo, chinthu chofunika kwambiri ndicho chitsanzo chanu. Bambo wina analankhula zimene makolo onse akudziwa pamene ananena kuti: “Ana sachita zimene mumanena; amachita zimene mumachita!”
2 Mlongo wina amene analeredwa ndi makolo oopa Mulungu ananena kuti: “Sitinayambepo tadzuka m’mawa tsiku Loweruka n’kufunsa ngati titi tipite mu utumiki kapena ayi. Tinkadziwa kuti tipita.” Nanunso mukhoza kuphunzitsa ana anu kuona kuti ntchito yolalikira n’njofunika mutakhala ndi chizolowezi chopita mu utumiki wa kumunda mlungu uliwonse monga banja. Sikuti zimenezi zimangothandiza anawo kuphunzira zinthu mwa kuona inuyo, komanso inuyo zimakuthandizani kuona maganizo awo, makhalidwe awo, ndi luso lawo.
3 Kuwaphunzitsa Pang’onopang’ono: Kuti ana azisangalala nawo utumiki, amafunika kuwakonzekeretsa n’cholinga choti azilalikira mogwira mtima. Mlongo amene tam’gwira mawu koyambirira uja ananenanso kuti: “Sikuti tinali kungotsatira makolo athuwo m’ntchito yawo ifeyo osakachitako chilichonse. Tinali kudziwa kuti tikatenga nawo mbali, ngakhale kukhale kungogogoda pakhomo n’kusiya kapepala kowaitanira ku msonkhano. Chifukwa choti tinali kukonzekera bwino zimene tidzachite Loweruka ndi Lamlungu, tinali kudziwiratu zimene tikalankhule.” Mungathe kuphunzitsa ana anu m’njira imeneyi mwa kupatula mphindi zingapo mlungu uliwonse kuwakonzekeretsa utumiki. Mwina mungachite zimenezi pa nthawi ya phunziro la banja kapena pa nthawi ina.
4 Kulalikira limodzi monga banja kumakupatsaninso mwayi wokhomereza choonadi mwa ana anu. Bambo wina wachikristu ankatenga mwana wake wamkazi akamapita kokagawira mathirakiti ku mudzi wina umene unali pa mtunda wa makilomita 10 kupita kokha. Mwanayo saiwala ndipo anafotokoza kuti: “Inali nthawi imeneyi pamene timayenda pamene bambo anga anakhomereza choonadi mu mtima mwanga.” (Deut. 6:7) Nanunso mukhale ndi dalitso ngati limeneli chifukwa chokhala ndi ndandanda ya banja lanu yolowera m’munda mlungu uliwonse.