Thandizani Ana Anu Kupita Patsogolo mu Utumiki
1 Makolo achikristu ali ndi udindo waukulu kwambiri wophunzitsa ana awo kutenga nawo mbali mu utumiki kuyambira ali aang’ono. Pali njira zambiri zimene makolo angagwiritse ntchito kuti athe kuchita zimenezi. Ana ena amatha kuloweza bwinobwino lemba la m’Baibulo ngakhale pamene sanaphunzire kuwerenga. Zimenezi zikhoza kukhala zochititsa chidwi kwambiri kwa omvera. Ndipo pamene anawo akukula, akhoza kuchita zambiri mu utumiki. Koma kodi makolonu, mungathandize bwanji ana anu kuti azitenga nawo mbali mu ulaliki? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kwambiri.
2 Mutamaliza kulonjerana, munganene kuti:
◼ “Mwana wangayu, [dzina lake], ali ndi lemba lothandiza kwambiri limene akufuna kukuuzani.” Mwanayo anganene kuti: “Lemba ili la Salmo landiphunzitsa dzina la Mulungu. [Mwanayo awerenge Salmo 83:18, kapena angonena mawu akewo.] Magazini awa akunena zimene Yehova Mulungu adzatichitire. Kodi ndingakusiyireni?” Ndiyeno mungamalizitse kukambiranako mwa kufotokoza mmene ntchito yapadziko lonse imeneyi imachirikizidwira.
3 Kapena mungayese njira iyi:
◼ “Muli bwanji? Ndikuphunzitsa mwana wangayu, [dzina lake], kukomera mtima anthu ena. Akufuna kukuuzani uthenga wachidule wa m’Baibulo.” Ndiyeno mwanayo anganene kuti: “Njira imodzi imene ndimakonda kuthandizira anthu ndiyo kuwauza chiyembekezo cha m’tsogolo chimene Baibulo limanena. [Mwanayo awerenge Chivumbulutso 21:4, kapena angonena mawu akewo.] Magazini awa akufotokozanso zimene Ufumu wa Mulungu udzatichitire. Ndikukhulupirira kuti musangalala kuwawerenga.”
4 Kugwiritsa ntchito ulaliki wosavuta nthawi zonse, kumathandiza ana kudzidalira pa luso lawo lolalikira uthenga wa Ufumu. Kuyeserera ulaliki maulendo angapo n’cholinga chofuna kuona mmene angalankhulire bwino ndiponso mmene angalankhulire ndi mawu amphamvu bwino kudzathandiza anawo kuti azitha kulankhula m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Kukonzekera bwino pasadakhale kuphatikizapo kuwayamikira mochokera pansi pa mtima, kudzathandiza ana aang’ono kufotokoza za chikhulupiriro chawo.
5 Ana ambiri, chifukwa chowalimbikitsa chonchi, ayenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa. N’zosangalatsatu kwambiri kuona ana athu akupita patsogolo mu utumiki wachikristu.—Sal. 148:12, 13.