Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/06 tsamba 5
  • Kubwereza Zophunziridwa pa Msonkhano Wadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza Zophunziridwa pa Msonkhano Wadera
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Kubwereza Zophunziridwa pa Tsiku la Msonkhano Wapadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kubwereza Zophunziridwa pa Msonkhano Wadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 2/06 tsamba 5

Kubwereza Zophunziridwa pa Msonkhano Wadera

Nkhani iyi mudzaigwiritse ntchito pa pulogalamu ya Msonkhano wa Utumiki pamene mpingo wanu watsala pang’ono kupita ku msonkhano wadera wa chaka cha utumiki cha 2006 ndiponso mutangobwera kumene kuchokera ku msonkhanowu. Woyang’anira wotsogolera adzakonza mmene mungachitire zimenezi mogwirizana ndi mmene unafotokozera Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2004, tsamba 4. Pobwerezapo, onetsetsani kuti mwafunsa mafunso onse, ndipo cholinga chachikulu chikhale kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimene zinafotokozedwa ku msonkhanowo.

TSIKU LOYAMBA

1. Kodi timavala bwanji umunthu watsopano, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kuuvala?

2. Kodi ena awonjezera bwanji nthawi yochitira ntchito yolalikira?

3. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudziyerekezera ndi anthu ena?

4. Kodi anthu m’banja angasonyeze bwanji umunthu watsopano m’banja mwawomo?

5. Kodi mu mpingo tingakhale bwanji okhulupirika?

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza umunthu watsopano mu utumiki wa kumunda?

7. Kodi kusinkhasinkha koyenera kumaphatikizapo chiyani, ndipo kodi kusinkhasinkha koteroko timapindula nako bwanji?

8. Kodi ndi makhalidwe ati omwe angatifewetse kuti Yehova athe kutiumba mosavuta m’manja mwake?

TSIKU LACHIWIRI

9. Kodi n’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito lilime lathu moyenera kuli kofunika?

10. Kodi timapindula bwanji tikamagwiritsa ntchito mawu abwino polankhulana ndi anzathu akuntchito, akusukulu, ndiponso anthu ena?

11. Kodi uphungu wa Paulo wopezeka pa Aefeso 4:25-32 tingaugwiritse ntchito bwanji pamene tikuchita zinthu ndi okhulupirira anzathu?

12. Kodi ndi njira iti yabwino kwambiri imene tingagwiritsire ntchito lilime lathu?

13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tigonjetse woipayo?

14. Kodi ndi mbali ziti zomwe tiyenera kuyesetsa kukhala osachitidwa mawanga ndi dziko?

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonza munthu wathu wam’kati tsiku ndi tsiku, ndipo kodi zimenezi tingazichite bwanji?

16. Kodi ndi uphungu wanji umene unaperekedwa pa msonkhano wadera wa chaka chino womwe mukufuna kugwiritsa ntchito?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena