Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Diso linapangidwa modabwitsa kwambiri. (Sal. 139:14) Koma ngakhale zili choncho, likhoza kuyang’ana chinthu chimodzi panthawi imodzi. Zimenezi n’zoona ponena za diso lenileni ndiponso diso lophiphiritsira. Kuti tithe kuona bwino mwauzimu, tiyenera kuika chidwi chathu chonse pa kuchita chifuniro cha Mulungu. Poona mmene zinthu zododometsa zikuchulukira m’dziko la Satanali, m’pake kuti mutu wa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wa chaka cha utumiki cha 2006 udzakhala wakuti “Khalanibe ndi Diso la Kumodzi.”—Mat. 6:22.
Kodi tingachite bwanji kuti tidzalandire madalitso a Yehova? (Miy. 10:22) Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yakuti, “Madalitso Amene Mungapeze Pokhalabe ndi Diso la Kumodzi.” Anthu amene adzawafunsa mafunso adzafotokoza mmene tingapindulire tikamagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba. Nkhani yoyamba imene adzakambe mlendo yakuti, “Kukhalabe ndi Diso la Kumodzi M’dziko Loipa,” idzatichenjeza za zinthu zimene zikhoza kusokoneza moyo wathu ndiponso zimene m’kupita kwa nthawi zikhoza kutsamwitsa moyo wathu wauzimu. Tidzaphunziranso zimene kusankha “dera lokoma” kumatanthauza.—Luka 10:42.
Kodi makolo ndiponso anthu ena angalimbikitse bwanji Akristu achinyamata kukhala n’chidwi ndi zolinga zauzimu? M’nkhani yakuti “Makolo Amene Amaponya Mivi Yawo Molunjika” ndi yakuti “Achinyamata Okhala ndi Zolinga Zauzimu,” makolo ndi achinyamata adzanenapo maganizo awo pa funso lofunika limeneli. (Sal. 127:4) Nkhani yomaliza imene adzakambe mlendo idzafotokoza mmene tingayenderebe limodzi ndi gulu la Yehova aliyense payekha, monga mabanja, ndiponso monga mpingo.
Ndiye kaya tangoyamba kumene kuphunzira choonadi kapena takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri, ndi bwino kuti ‘tikhalebe ndi diso la kumodzi.’ Choncho, pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera idzatithandiza kuti tichite zimenezi.