Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo Achidule Pakhomo ndi pa Telefoni
1, 2. Kodi pulogalamu yathu yophunzitsa Baibulo tingaisinthe bwanji kuti tithandize anthu amene amakhala otanganidwa?
1 Anthu n’ngotanganidwa masiku ano. Koma ngakhale zili choncho, ambiri ali ndi chidwi ndi zinthu zauzimu. Ndiyeno kodi tingatani kuti tikhutiritse chikhumbo chawo cha zinthu zauzimucho? (Mat. 5:3) Ofalitsa ambiri amatha kuphunzira Baibulo ndi anthu mwachidule pakhomo kapena pa telefoni. Kodi mungawonjezere utumiki wanu mwa kuchita zimenezi?
2 Kuti tiyambitse maphunziro a Baibulo, tiyenera kukhala okonzeka kusonyeza ena mmene timaphunzirira Baibulo paliponse pamene mpata wapezeka. Kodi zimenezi tingazichite bwanji, ndipo tingazichite kuti?
3. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza munthu mmene timaphunzirira Baibulo paulendo woyamba, ndipo kodi zimenezi tingazichite bwanji?
3 Phunziro Lachidule: Mukakumana ndi munthu amene akufunitsitsa kuti mukambirane naye za Baibulo, ingotsegulani pa ndime imene inuyo mwaikonzekera kale, mwachitsanzo ndime yoyamba ya phunziro 1 mu bulosha la Mulungu Amafunanji. Mukatero werengani ndimeyo, funsani funso lakelo, ndipo kambiranani malemba osagwidwa mawu, limodzi kapena awiri. Mungachite zimenezi mwachidule kwa mphindi zisanu kapena khumi. Ngati munthuyo wasangalala nako kukambiranako, konzani zoti nthawi ina mudzakambiranenso ndime imodzi kapena ziwiri zotsatira.—Mfundo zina zokhudza mmene mungayambitsire maphunziro mwachindunji mungazipeze mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002, tsa. 6.
4. Kodi tingayambitse bwanji phunziro la Baibulo lachidule pamaulendo obwereza?
4 Mukhozanso kugwiritsa ntchito njira yomweyi kuyambitsira maphunziro a Baibulo popanga maulendo obwereza. Mwachitsanzo, mukhoza kusonyeza bulosha la Mulungu Amafunanji ndiyeno n’kukambirana za dzina la Mulungu pogwiritsa ntchito phunziro 2, ndime 1 ndi 2. Paulendo wotsatira, mukhoza kudzakambirana ndime 3 ndi 4 pa nkhani yokhudza zimene Baibulo limanena zokhudza makhalidwe a Yehova. Paulendo winanso, mukhoza kudzakambirana ndime 5 ndi 6 ndiponso chithunzi cha patsamba 5 kufotokoza mmene kuphunzira Baibulo kumatithandizira kum’dziwa Yehova. Zonsezi zikhoza kumachitika mwachidule.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amakonda kuphunzira Baibulo kudzera pa telefoni? (b) Kodi tingagwiritse ntchito njira iti pamene tikupempha anthu kuphunzira nawo kudzera pa telefoni?
5 Pa Telefoni: Anthu ena angakonde kwambiri kuphunzira Baibulo kudzera pa telefoni kusiyana n’kuti awirinu muzikhala pansi n’kumaphunzira. Tamvani chokumana nacho ichi: Mlongo wina akuchita ulaliki wa nyumba ndi nyumba, anakumana ndi mayi wina wachitsikana amene ali ndi ana komanso amagwira ntchito yosapereka mpata wokwanira wopumula. Mlongoyo ataona kuti mayiyo sakum’pezanso panyumba, anaganiza zongomuimbira telefoni. Mayiyo anafotokoza kuti n’zoona kuti sangapezedi nthawi yoti n’kumakambirana za Baibulo. Ndiyeno mlongoyo anati: “Pa mphindi 10 kapena 15 zokha basi, mukhoza kuphunzira kanthu katsopano ngakhale kudzera pa telefoni.” Mayiyo anayankha kuti: “Chabwino, ngati ndi pa telefoni, ndiye zili bwino.” Posakhalitsa, phunziro lokhazikika linayamba kumachitika kudzera pa telefoni.
6 Kodi alipo ena amene mumawayendera omwe angakonde kumaphunzira kudzera pa telefoni? Mukhoza kuyesa njira imene tangofotokoza kumeneyi, kapena mukhoza kungonena kuti: “Ngati mungakonde, tikhoza kumakambirana za Baibulo kudzera pa telefoni. Kodi zingakhale bwino kwa inu?” Mwa kusintha pulogalamu yathu yophunzitsa Baibulo mogwirizana ndi moyo wa ena, tikhoza kuwathandiza, “kum’dziwadi Mulungu.”—Miy. 2:5; 1 Akor. 9:23.