Chititsani Maphunziro a Baibulo Achidule Ndiponso a Patelefoni Opita Patsogolo
1. Kodi cholinga chathu n’chiyani pochititsa maphunziro a Baibulo?
1 N’chinthu chosangalatsa kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo! Komabe, kupeza munthu amene ali ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo n’chiyambi chabe. Cholinga cha phunzirolo n’kuthandiza munthuyo kuti akhale wophunzira weniweni wa Kristu. (Mat. 28:19, 20) Kodi n’chiyani chingatithandize kukwanitsa cholinga chimenecho?
2. Kodi maphunziro a Baibulo achidule ndi a patelefoni ndi otani, ndipo n’chifukwa chiyani amathandiza?
2 Anthu ndi Otanganidwa: Masiku ano anthu amakhala otanganidwa kwambiri. M’madera ena, ndi anthu ochepa okha amene pachiyambi pomwe angalole kupatula ola lathunthu kuti aziphunzira Baibulo. Kuti tithandize anthu oterewa, talimbikitsidwa kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo achidule kapena a patelefoni. Poyamba, maphunziro oterewa angakhale osatenga nthawi yaitali ndipo tikhoza kungophunzira mavesi owerengeka okha a m’Baibulo pogwiritsa ntchito ndime imodzi kapena ziwiri za m’buku ngati la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. N’zoyamikirika kwambiri kuti ofalitsa ambiri panopa akuchititsa maphunziro oterewa achidule kapena a patelefoni.
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kusintha kuti tisiye kuchititsa phunziro lachidule n’kuyamba lalitali?
3 Koma kodi tiyenera kukhutira n’kuchititsa phunziro lachidule mpaka kalekale? Ayi. Ngakhale kuti ndi bwino kuti tisamakhalitse munthu akatilola kulankhula naye tikangoyambitsa kumene phunziro, Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 1990 pa tsamba 8 unanena kuti: “Mukakhazikitsa phunzirolo ndipo chidwi cha munthuyo chikawonjezeka, mukhoza kumakhala nthawi yotalikirapo pochititsa phunzirolo.” Zimenezi n’zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, mwana amene wakhala nthawi yaitali osadya poyamba mukhoza kumam’patsa tizakudya tochepa mpaka chilakolako chake chofuna kudya chitabweranso, koma sitingayembekezere kuti apeza mphamvu zokwanira ndi kukula bwino ngati atamadya tizakudya tochepato kwa miyezi yambirimbiri. Mofanana ndi zimenezi, wophunzira Baibulo amafunika phunziro lalitali bwino ndiponso lochitika nthawi zonse kuti akule n’kufika pokhala mtumiki wa Mulungu wokhwima maganizo.—Aheb. 5:13, 14.
4. Kodi ubwino wochitira m’nyumba phunziro la Baibulo ndi wotani?
4 Maphunziro a Baibulo Aatali: Ndi bwino kuchitira phunziro la Baibulo pamalo abata, monga m’nyumba kapena pa malo ena abwino. Malo oterowo amathandiza kuti munthu aphunzire bwino ndiponso amvetsetse Mawu a Mulungu. (Mat. 13:23) Zingathandizenso mphunzitsiyo kuti azigwirizanitsa bwino nkhaniyo ndi zosowa za wophunzirayo. Ndiponso, kukhala ndi phunziro lotalikirapo kungathandize kuti muphunzire Mawu a Mulungu mwatsatanetsatane, m’njira yolimbitsa chikhulupiriro.—Aroma 10:17.
5. Kodi tingatani kuti tisiye kuchititsa phunziro lachidule n’kuyamba lalitali?
5 Kodi mungatani kuti musiye kuchititsa phunziro lachidule n’kuyamba lalitali? Mukachititsa phunziro lachidule maulendo angapo, bwanji osangomufunsa munthuyo ngati mungathe kuphunzira naye kwa nthawi yotalikirapo, n’kumuuza kutalika kwake? Kapena mungachite zimenezi mwanjira ina pomufunsa munthuyo kuti, “Kodi lero mungakhale ndi nthawi yotalikirapo kuti tikambirane zimenezi?” kapena “Kodi lero mungakonde kuti tikambirane nkhani imeneyi kwa nthawi yaitali bwanji?” Ngati kuyesayesa kwanu sikunaphule kanthu, pitirizanibe kukhala ndi maphunziro achidule. Pa nthawi yoyenerera, dzayesereninso kusintha kuti likhale lotalikirapo.
6. Kodi tizichita utumiki wathu n’cholinga chotani, ndipo malangizo a mu nkhani ino angatithandize bwanji kukwaniritsa cholinga chimenecho?
6 Pamene tikupitiriza kufunafuna anthu achidwi, tiyeni tisaiwale cholinga chathu choyambitsira ndi kuchititsira maphunziro a Baibulo. Cholinga chathu n’kuthandiza anthu oona mtima kuti akhale atumiki a Yehova odzipereka ndi obatizidwa. Yehova adalitse khama lathu pamene tikuchita utumiki wathu n’cholinga chimenechi.—2 Tim. 4:5.