Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2006 Wakuti “Chipulumutso Chayandikira”
1. Kodi anthu akale a Mulungu ankasonyeza motani kuti akuyamikira kulambira koona, ndipo ndi mwayi wotani wofanana ndi umenewo umene tili nawo masiku ano?
1 Mfumu Hezekiya ya ufumu wakale wa Yuda inatuma anthu a mtokoma kukapereka pamanja makalata a uthenga woitanira anthu ku msonkhano ku Yerusalemu. (2 Mbiri 30:6, 13) Mmene anthu ankalandirira uthengawo, zimatiuza zambiri ponena za maganizo awo pankhani ya kulambira koona. (2 Mbiri 30:10-12) M’miyezi ikubwerayi, atumiki a Yehova amakono adzakhala ndi mwayi wofanana ndi umenewo wosonyeza kuti amayamikira kuchokera pansi pamtima mpata wosonkhana pamodzi kuti alambire Yehova. Kodi inuyo mudzapita ku Msonkhano Wachigawo wa chaka chino wakuti “Chipulumutso Chayandikira”?
2. Kodi n’chiyani chimene tingachite panopo kuti tikapindule mokwanira ndi msonkhano?
2 Konzekani Pakali Pano: Kuti tikapindule mokwanira ndi pulogalamu yauzimu imene akutikonzera mokoma mtima, tifunikira kukonza zokapezeka pa msonkhano wonse. Ndi nzeru kuti muyambiretu pakali pano kukonzekera inuyo ndi banja lanu kuti mukapezekeko masiku onse atatu. (Miy. 21:5) Pokonzekera, mungafunike kupempheratu tchuthi ku ntchito, kukambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu amene si Mboni, ndi kuthandiza anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo kuti akapezekeko masiku onse atatu. Musanyalanyaze zinthu zofunikira zimenezi kuti mudzazipange nthawi itatha. M’malo mwake, pempherani kwa Yehova ndi kukhulupirira kuti chimene tingapemphe, iye ‘adzachichita.’—Sal. 37:5.
3, 4. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira makonzedwe amene apangidwa a malo ogona?
3 Malo Ogona: Kuyamikira khama la abale athu omwe agwira ntchito modzipereka pothandiza kukonza malo ogona, kuganizira za anthu ena amene adzapezeke pamsonkhano, ndiponso kulemekeza kakonzedwe ka gulu la Mulungu, kudzatilimbikitsa kuti titsatire malangizo onse amene aperekedwa mu nkhani ino.—1 Akor. 13:5; 1 Ates. 5:12, 13; Aheb. 13:17.
4 Nthawi zambiri abale amakonza okha zokakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’madera omwe mukuchitikira msonkhano. M’midzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’midadada yomwe antchito odzipereka pamsonkhanopo amanga. Pamisonkhano ina, ena amagona m’nyumba zogona ana asukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu ndi kukhalabe komweko masiku ena n’cholinga choti muchite tchuthi msonkhanowo utatha. Malo ogona amenewo ndi anthawi ya msonkhano yokha basi. Amene apatsidwa malowo azionetsetsa kuti iwo pamodzi ndi ana awo akuchita ulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapenanso kulowa malo osayenera iwo kulowamo. Ngati pali zina zimene eninyumba zikuwavuta pankhaniyi, aziuza msanga Dipatimenti Yoona za Malo Ogona pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
5. Kodi mungathandize motani anthu amene ali ndi zosowa zapadera?
5 Zosowa Zapadera: Lemba la Miyambo 3:27 limati: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” Kodi mungawachitire bwanji ena zabwino pa nthawi ya msonkhano wachigawo? Ofalitsa omwe ndi okalamba, odwala, atumiki a nthawi zonse, ndi enanso angafunikire kuthandizidwa pankhani ya kayendedwe ndi malo ogona. Achibale a anthu amenewa ndiwo ali ndi udindo woyambirira wowathandiza. (1 Tim. 5:4) Ngati sangatero, abale ndi alongo akhoza kuwathandiza. (Agal. 6:10) Oyang’anira maphunziro a buku ayenera kufufuza kwa amene ali ndi zosowa zapadera m’gulu lawo kuti atsimikize ngati akonzekera zonse bwinobwino nthawi idakalipo.
6. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupita ku msonkhano umene mpingo wathu wagawiridwa? (b) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati pa zifukwa zina mufunika kupita ku msonkhano wosiyana ndi umene mumafunikira kupita?
6 Kupita ku Msonkhano Wina: Pofuna kuonetsetsa kuti malo okhala, mabuku, malo ogona, ndi zina zotero n’zokwanira, tikukulimbikitsani kupita ku msonkhano umene mpingo wanu wagawiridwa. Koma ngati kungakhale kovuta kukapezeka kumeneko ndipo mukufuna kudzapita ku msonkhano wina, tikukupemphani kuti mulankhule ndi mlembi wa mpingo wanu kuti akupatseni adiresi ya ku msonkhano womwe mukufuna kudzapitawo. Ngati malo amenewo kudzachitike misonkhano ingapo, sonyezani madeti a msonkhano womwe mukufuna kudzapitawo.
7. Kodi tingathandize mwa njira ina iti kuti msonkhano umene ukubwerawu udzakhale wosangalatsa?
7 Antchito Odzipereka: Sitikukayika m’pang’ono pomwe kuti onse amene adzafike pamsonkhano ndi kupindula ndi chakudya chauzimu, ndi kukhala ndi mpata wolimbikitsana pocheza adzasangalala kwambiri. Chimwemwe chathu chingakhalenso chachikulu koposa, ngati titadzipereka kukagwira ntchito imene ingathandizire kuti msonkhano udzayende bwino. (Mac. 20:35) Komiti ya Msonkhano ya kwanuko posachedwapa iyamba kuitana anthu oti akathandize nawo pa ntchito imeneyi. Kodi mungadzipereke kukathandiza nawo pa ntchitoyi?—Sal. 110:3.
8. Kodi n’chiyani chimene mumayamikira ponena za misonkhano yachigawo ya chaka ndi chaka, ndipo n’chiyani chimene muyenera kutsimikiza mtima kuchita?
8 Ali pamsonkhano wachigawo, mnyamata wina wa zaka zisanu anati: “Msonkhano wachigawo ndi mbali imene ndimakonda kwambiri pa kulambira Yehova.” Kuyamikira kochokera pansi pa mtima kotere kumatikumbutsa za chimwemwe chimene timakhala nacho kumsonkhano wachigawo wa chaka ndi chaka. Zilidi monga mmene wamasalmo anaimbira kuti: “Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.” (Sal. 84:10) Davide anafotokoza maganizo ake poimba kuti: ‘Ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kotero kuti ndipenye kachisi wake.’ (Sal. 27:4) Davide anali wosangalala kwambiri kukhala pakati pa olambira Yehova. Nafenso tingasonyeze kuti timayamikira kulambira koona mwa kukapezeka masiku onse atatu pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.”
[Bokosi patsamba 4]
Nthawi za Pulogalamu
Lachisanu ndi Loweruka
8:30 a.m. - 4:05 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. - 3:10 p.m.