Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/05 tsamba 7
  • Sukulu Imene Imatithandiza Kugwiritsa Ntchito Zomwe Taphunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu Imene Imatithandiza Kugwiritsa Ntchito Zomwe Taphunzira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Timapindulira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Kumveketsa Phindu la Nkhani Yanu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kukonzekera Nkhani Zokambira Mpingo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 12/05 tsamba 7

Sukulu Imene Imatithandiza Kugwiritsa Ntchito Zomwe Taphunzira

1 Pamene tikugwiritsa ntchito zimene zalembedwa mu Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2006, tikufuna kupindula ndi ziphunzitso za m’Malemba pozigwiritsa ntchito mu utumiki wathu wopatulika ndiponso pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Timayesetsa kuchita zimene tikuphunzira.—Yoh. 13:17; Afil. 4:9.

2 Kupereka Ndemanga: M’ndandanda ya chaka chino aikamo mphindi imodzi yowonjezera kuti omvera azipereka ndemanga pa mfundo zazikulu za Baibulo. Zimenezi zikutanthauza kuti mbale amene akupereka mfundo zazikulu ayenera kusamala kuti amalize mbali yake mu mphindi zisanu m’malo mwa mphindi sikisi. Amene akupereka ndemanga ayenera kusamala za nthawi. Mwa kuganiza kaye pasadakhale, munthu amene akupereka ndemanga angathe kulongosola mfundo zothandiza kwa masekondi 30 kapena kucheperapo. Choncho pafupifupi anthu khumi angapereke ndemanga zaphindu mu mphindi zisanu zimene azipereka kwa omvera kuti alankhulepo.

3 Nkhani Zophunzitsa: Mfundo zazikulu za Baibulo ndi nkhani yolangiza zizikhala zonena za ubwino wake wa mfundo za m’nkhanizo mu utumiki wathu ndi mbali zina za moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Wokamba nkhani sayenera chabe kungopangitsa omvera kulakalaka kuchita zomwe akulankhulazo ayi. Koma, ayenera kutchula zinthu zimene zikufunikira kuti omvera achite, ndi kusonyeza mmene angachitire, ndiponso kukamba za phindu limene tingapeze potsatira zimenezo. Wokamba nkhaniyo anganene kuti, “Lembali likutithandiza motere,” kapena “Tingagwiritse ntchito motere mavesi amenewa mu utumiki.” Akulu ndi atumiki othandiza amene akudziwa mmene zinthu zilili kwawoko ayenera kuyesetsa kufotokoza mwachindunji mmene aliyense angagwiritsire ntchito mfundo zimene iwo akukambazo.

4 Kutchula zitsanzo za m’Baibulo kungakhale kogwira mtima makamaka pofotokoza mmene tingagwiritsire ntchito zimene taphunzira. Pambuyo potchula chitsanzo cha m’Malemba, wokamba nkhani anganene kuti, “Mwina inunso mungakumane ndi zimenezi.” Ayenera kuonetsetsa kuti mulimonse mmene akugwiritsira ntchito chitsanzo cha m’Baibulo, zikugwirizana ndi mfundo zina zozungulira pamene watengapo chitsanzocho m’Baibulomo, ndipo zikugwirizana ndi Baibulo lonse, ndiponso ndi zimene wafalitsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mat. 24:45.

5 Nzeru zimatanthauza kugwiritsa bwino ntchito zimene ukudziwa ndi kuzindikira. “Nzeru ipambana.” (Miy. 4:7) Pamene tikupitirizabe kupeza nzeru yeniyeni kuchokera mu maphunziro athu a m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, tiyeni tiwonjezere luso lathu lophunzitsa ena nzeru imeneyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena