Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Anthu ambiri akuda nkhawa kuona kuti nyengo ino ya chikondwerero yakhala yopangira malonda. Kodi mukuganiza kuti anthu sakulemekezanso nyengoyi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza za kusintha kwa miyambo ya chikondwerero chimenechi. Ikufotokozanso za mmene tingalemekezeredi Mulungu ndi Kristu.” Ndiyeno werengani Yohane 17:3.
Galamukani! Dec. 8
Anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu amakonda kwambiri mtundu wawo kuposa mitundu ina, koma kodi zimenezo n’zogwirizana ndi Baibulo? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Machitidwe 10:34.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Anthu atha kuchita zinthu zabwino, koma ngakhale zili choncho iwo nthawi zambiri amachita zinthu zoipa kwambiri. Kodi mumadziwa chifukwa chake? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi yankho lochokera m’Baibulo. Ikufotokozanso za mmene ubwino udzagonjetsera kuipa posachedwapa.” Ndiyeno werengani Aroma 16:20.
Galamukani! Dec. 8
Achinyamata ambiri amene ali pachibwenzi ndipo akufuna kukwatirana amadzifunsa kuti, ‘Kodi tichite kukhala ndi mwambo wonse wa ukwati pofuna kulowa m’banja?’ Kodi mukuganiza chingawathandize n’chiyani kuchita zimene iwo ndi achibale awo angasangalale nazo? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zimene zingathandize achinyamata pa nkhani imeneyi ndiponso mfundo yaikulu imene achinyamata oopa Mulungu sayenera kuiwala. Ndiyeno werengani 1 Akorinto 10:31.