Sonyezani Ena Chidwi Powafunsa Mafunso ndi Kumvetsera Zonena Zawo
1 Anthu ambiri amasangalala kunena maganizo awo pa nkhani inayake koma sasangalala kuti aziuzidwa zinthu mokhala ngati kuti iwowo sadziwa kanthu. Sasangalalanso kuwafunsa mafunso ngati kuti ali m’khoti. Motero, atumiki achikristufe tiyenera kukhala ndi luso lofunsa anthu mafunso m’njira yowalimbikitsa kunena maganizo awo.—Miy. 20:5.
2 Mafunso athu sayenera kuopseza anthu ayi, koma ayenera kuwalimbikitsa kuganizira mozama zimene tikukambirana nawo. Mbale wina akamalalikira nyumba ndi nyumba amafunsa kuti, “Kodi mukuganiza kuti nthawi inayake anthu adzayamba kupatsana ulemu ndiponso kulemekezana?” Malingana ndi mmene munthuyo wayankhira, mbaleyu amapitiriza kunena kuti, “Kodi mukuganiza kuti pakufunika chiyani kuti zimenezi zitheke?” kapena “N’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?” Pa ulaliki wamwamwayi ndiponso polalikira m’malo opezeka anthu ambiri, mbale wina amafunsa anthu amene ali ndi ana kuti, “Kodi n’chiyani chimakusangalatsani kwambiri monga kholo?” Kenaka amafunsa kuti, “Kodi ndi zinthu zotani zimene zimakudetsani nkhawa kwambiri?” Mungathe kuona kuti mafunso amenewa amalimbikitsa anthu kunena maganizo awo popanda kuwachititsa manyazi. Tiyenera kusintha mafunsowa ndiponso kafunsidwe kake mogwirizana ndi gawo lathu.
3 Alimbikitseni Kunena Maganizo Awo: Ngati anthu akufuna kukuuzani maganizo awo, mvetserani moleza mtima ndipo musawadule pakamwa. (Yak. 1:19) Vomerezani kuti mukumvetsa zimene akunena. (Akol. 4:6) Mungathe kuwayamikira pa mfundo zawozo ngati zili zoti mungaziyamikiredi moona mtima. Afunseni mafunso ena kuti mudziwe zimene akuganiza ndiponso chifukwa chimene akuganizira choncho. Yesetsani kupeza mfundo zimene nonse mungathe kugwirizana nazo. Mukafuna kuwerenga lemba, mungafunse kuti, “Kodi munayamba mwaganizirapo ngati izi zili zotheka?” Pewani kuchita liuma kapena kupikisana mawu.—2 Tim. 2:24, 25.
4 Mafunso athu amakhudza kwambiri anthu, ngati ifeyo tikumvetsera zonena zawo. Anthu amadziwa kuti tikumvetsera moona mtima kapena ayi. Woyang’anira woyendayenda wina anati, “Mukamamvetsera zonena za anthu moleza mtima, anthuwo amakopeka nanu kwambiri ndipo amadziwa kuti mukuwaganiziradi.” Tikamamvetsera ena akamanena maganizo awo, timasonyeza kuti tikuwalemekeza, motero zimenezi zingawalimbikitse kumvetsera uthenga wabwino umene timafuna kuuza anthu.—Aroma 12:10.