Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu woyambira January 9
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 20: Mbali Zatsopano mu Galamukani! Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani za kusintha kwa Galamukani! monga mmene tinalengezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2005, patsamba 1, ndime 5 ndi 6. Phatikizanipo mfundo zotengedwa m’nkhani yakuti “Kwa Owerenga” ya mu Galamukani! ya January 2006, masamba 3 ndi 4. Tchulani zitsanzo zotsimikizira kuti magazini imeneyi mosapita m’mbali imasonyeza owerenga zimene zili m’Baibulo. Pemphani omvera kupereka ndemanga zawo pa mbali yatsopano yomwe ili pa tsamba 31 ya magaziniyi. Tipitirizabe kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pamodzi pa ulendo woyamba. N’zachidziwikire kuti tsopano tizigawira magazini imodzi yokha ya Galamukani! kwa onse amene timakawapatsa magazini ndi onse amene amakonda kuwerenga magazini athu. Pogwiritsa ntchito zitsanzo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya January 15 ndi Galamukani! ya January. Mungathe kugwiritsanso ntchito zitsanzo zina zoyenererana ndi kwanuko. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 20: “Achinyamata Amene Akuwala Monga Zounikira.”a Pemphani achinyamata kuti anene mmene akhala akulalikirira kusukulu. Mungathe kukonzeratu zoti wachinyamata mmodzi kapena awiri adzalankhulepo za mmene akhala akulalikirira kusukulu.
Nyimbo Na. 125 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Limbikitsani aliyense kuwerenganso Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, masamba 14 mpaka 24 pokonzekera nkhani yokambirana imene idzachitike milungu iwiri ikubwerayi pa Msonkhano wa Utumiki.
Mph. 15: “Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Ndilo tiziphunzitsira anthu.”b Limbikitsani omvetsera kuti akhale ndi chilakolako chofuna kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi buku latsopanoli.
Mph. 20: “Mmene Mungayambitsire Maphunziro M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.” Nkhani yokambirana ndi omvetsera yokhala ndi zitsanzo yochokera pa tsamba 3 la mphatika. Tingayambe tsopano lino kugwiritsira ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani poyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu achidwi. Konzani zoti pakhale zitsanzo zitatu zokonzekeredwa bwino zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito (1) tsamba 4 ndi 5, (2) tsamba 6, ndi (3) ndime yoyamba patsamba 7 poyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo wobwereza. Musanachite chitsanzo chilichonse, longosolani kaye mfundo zikuluzikulu za chitsanzocho ndipo pamapeto pa chitsanzocho gogomezeraninso mfundo zikuluzikuluzo. Ndime za m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani mungathe kuzichita mwachidule ngati pakufunika kutero. Pomaliza chitsanzo chilichonse wofalitsa azipangana ndi mwininyumba tsiku loti adzabwerenso.
Nyimbo Na. 107 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndiponso ndalama zimene zaperekedwa mumpingomo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya February. Wachinyamata achite chitsanzo chimodzi. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 15: Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera tsamba 4 mpaka 7 m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Mawu oyamba ozikidwa pa tsamba 4 asapitirire mphindi zitatu ndipo kenaka kambiranani ndi omvetsera tsamba 5 ndi 6. Pa Misonkhano ya Utumiki ya m’tsogolo tidzakambirana mbali zina za buku la Gulu.
Mph. 20: “Sonyezani Ena Chidwi Powafunsa Mafunso ndi Kumvetsera Zonena Zawo.”c Pokambirana ndime 2, funsani omvetsera kuti anene mafunso amene aona kuti n’ngothandiza poyambitsa kukambirana. Sonyezani mmene mungalimbikitsire munthu kunena maganizo ake pomufunsa mafunso oyenerera ndi kumvetsera mwachidwi akamayankha.
Nyimbo Na. 205 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 30
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa January. Tchulani mabuku ogawira mwezi wa February, ndipo onetsani chitsanzo chimodzi cha momwe tingagawire mabukuwo.
Mph. 15: Mphatso Zachikondi Zotipindulitsa. Ikambidwe ndi mkulu. Werengani ndi kukambirana kalata ya pa January 3, 2006, yochokera ku ofesi ya nthambi kupita ku mipingo yonse yolongosola za njira zimene tingapindulire ndi ntchito ya Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC) ndiponso Gulu Lozonda Odwala (PVG).
Mph. 22: “Kodi Mwana Wanu Angathe Kusankha Zinthu Mwanzeru?” Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, kenaka kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu. Mbale wodziwa kuwerenga bwino awerenge mokweza ndime iliyonse. Kambiranani malemba onse osonyezedwa m’nkhaniyi. Mukakambirana ndime 2, yerekezerani nkhani za achinyamata awiri amene anatchulidwa mu ndime 16 ndi 17 ndiponso mu kabokosi ka patsamba 16 ndi 17 mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1991. Pomaliza, limbikitsani makolo kuti awerenge nkhani yonseyo ndi kuti akamaliza akambirane ndi ana awo za lamulo la Baibulo pankhani ya magazi, ndiponso ayeserere zinthu zosiyanasiyana zowathandiza anawo kulankhula mochoka pansi pamtima akamafotokoza za chikhulupiriro chawo. Mitu ya banja iyenera kuonetsetsa kuti mwana aliyense wobatizidwa akuyenda ndi khadi yake ya DPA ndi kuti mwana aliyense osabatizidwa ali ndi Khadi la Mwana. Nthawi zonse munthu akagonekedwa m’chipatala n’kupezeka kuti pabuka nkhani ya magazi, akulu ayenera kudziwitsa Komiti Yolankhulana ndi Achipatala.
Nyimbo Na. 45 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 6
Mph. 8: Zilengezo za pampingo.
Mph. 25: Kudziwa Bwino Buku Lathu Latsopano Lophunzitsira. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Pemphani omvetsera kuti anene zinthu zimene akuyamikira za buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, monga mafunso oyambirira ndiponso bokosi limene limalongosola mfundo zikuluzikulu za chaputala chilichonse (tsamba 106, 114); zithunzi (tsamba 122 ndi 123, 147, 198); ndiponso mawu a kumapeto kwa bukuli (tsamba 197, ndime 1 ndi 2). Bukuli limalongosola zinthu mwansangala ndiponso mokopa (tsamba 12, ndime 12). Limalongosola zinthu m’njira yosavuta kumva (tsamba 58, ndime 5) ndipo lili ndi zitsanzo zogwira mtima kwambiri (tsamba 159, ndime 12). Mawu oyamba a bukuli anawakonza moti atithandize kuyambitsa maphunziro a Baibulo (tsamba 3 mpaka 7). Khalani ndi chitsanzo cha mmene tingagwiritsire ntchito bokosi la patsamba 7 ndi wophunzira Baibulo watsopano. Nenani zinthu zimene anthu akumana nazo pogwiritsa ntchito buku latsopanoli.
Mph. 12: Upainiya Wothandiza Umabweretsa Madalitso. (Miy. 10:22) Uzani anthu amene anachita upainiya wothandiza chaka chatha kuti anene mmene anakonzera ndandanda yawo kuti athe kuchita upainiya ndiponso auzeni kuti alongosole chimwemwe ndiponso madalitso amene apeza chifukwa chochita upainiyawu. Limbikitsani onse kuti aganizire ndiponso apemphere kwa Yehova za nkhani yodzachita upainiya wothandiza mu March, April, ndi May.
Nyimbo Na. 16 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.