Zimene Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr.15
“Pafupifupi aliyense amavomereza kuti chinsinsi cha moyo wa banja losangalala chagona pa kulankhulana bwino, komabe anthu ambiri amavutika kuti alankhulane bwino. Kodi mukuganiza kuti chimapangitsa zimenezi n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza anthu kulankhulana bwino.” Werengani Yakobo 1:19.
Galamukani! Apr.
“Anthu ambiri amanena kuti mtanda umawathandiza kuyandikira kwa Mulungu. Komabe, ena amadabwa kuti: Kodi n’koyenera kulambira chinthu chimene anapherapo Yesu? Kodi Yesu anaferadi pamtanda? Nkhani imene yayambira patsamba 12, ikuyankha mafunsowa mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.” Werengani Machitidwe 5:30.
Nsanja ya Olonda May 1
“Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi amavutika chifukwa cha umphawi. Kodi mukuganiza kuti anthu amenewa angathandizidwe bwanji? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani 1 Petro 2:21.] Magazini iyi ikufotokoza mmene tingatsatirire chitsanzo cha Yesu podera nkhawa anthu osauka.”
Galamukani! May
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani timakalamba? [Yembekezani ayankhe.] Zimene Baibulo limalongosola zokhudza chifukwa chimene timakalambira, zimasonyeza zomwe Mulungu wachita kuti tidzathe kukhala ndi moyo wosatha. [Werengani Yesaya 25:8.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza mfundo zina zatsopano zomwe anthu atulukira zokhudza kukalamba.”