Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/09 tsamba 8
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 4/09 tsamba 8

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda April 1

“Anthu ena amakhulupirira kuti zimene zimatichitikira zinalembedweratu, pamene ena amaganiza kuti timachita kusankha tokha. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Onani mfundo yochititsa chidwi iyi. [Werengani Mlaliki 9:11.] Nkhaniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa funso lakuti, ‘Kodi Mulungu analemberatu zomwe zidzachitikire munthu aliyense?’ Ndipo asonyezeni nkhani yomwe ili patsamba 26.

Galamukani! April

“Mabanja ambiri amatha chifukwa cha kusakhulupirika. Kodi mukuganiza kuti kugwiritsa ntchito lemba ili kungathandize kuti mabanja asamathe? [Werengani Mateyo 5:28. Ndipo yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ili ndi mfundo za m’Baibulo zothandiza mabanja kukhala okhulupirika.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 28.

Nsanja ya Olonda May 1

“Kodi n’chiyani chingalepheretse munthu kukhulupirira Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Mogwirizana ndi lemba ili, chikhulupiriro n’chofunika. [Werengani Aheberi 11:6.] Magaziniyi ikufotokoza njira zinayi zimene tingatsatire kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.”

Galamukani! May

“Anthu ambiri masiku ano akugwiritsa ntchito mankhwala olandira kuchipatala molakwika. Kodi mukuganiza kuti chikuchititsa n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatchula chifukwa chachikulu chimene chikuchititsa zimenezi, makamaka kwa ana. [Werengani Miyambo 13:20.] Magaziniyi iyi ili ndi mfundo zimene zingathandize inuyo ndi banja lanu kupewa vutoli.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena