Branch Letter
Okondedwa Ofalitsa Ufumu Nonse:
Tikufuna tikuyamikireni kwambiri chifukwa chothandiza nawo modzipereka pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’gawo la nthambi yathu kuyambira pamene ntchitoyi inayamba mu 1998. Panopa, Nyumba za Ufumu 867 zamangidwa. (Sal. 110:3) Pakadali pano pali magulu eyiti omanga Nyumba za Ufumu amene akuyang’anira ntchito zosiyanasiyana m’gawo la nthambi yathu.
Kodi n’chiyani chimafunika kuti Nyumba ya Ufumu imangidwe? Abale ndi alongo, kuphatikizapo ana, amathandiza pa ntchito youmba ndi kuotcha njerwa. Komanso, ntchito yomanga isanayambe, abale amadzipereka kukumba maziko a nyumba, kukumba zimbudzi, ndipo nthawi zina amatuta mchenga ndi miyala. Alongo amathandiza popanga konkire, kuperekera njerwa, ndi kuphika. Anthu onsewa amasonyezadi mzimu wodzimana pothandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’Malawi muno. (Aheb. 6:10) Anthu ena salephera kuona chikondi ndi mgwirizano zimene zimakhalapo pomanga Nyumba za Ufumu, monga momwe chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.
M’Chigawo Chapakati, anthu okhala pafupi ndi malo amene pamamangidwa Nyumba ya Ufumu anadabwa poona momwe ntchitoyo inali kuyendera mofulumira. Anati sanaonepo anthu akugwira ntchito mogwirizana ngati momwe abale ndi alongo athuwo anali kuchitira. Mwamuna wina mpaka ananena kuti: “Anthu a Mboni za Yehova mumakondanadi, ndipo mumatsatiradi mfundo za m’Baibulo.” Amfumu a m’mudzimo anati anthu onse m’mudzimo akanakhala ngati Mboni za Yehova, bwenzi zinthu zili bwino kwambiri. Akazi a amfumuwo nthawi zina ankakathandiza nawo ntchitoyo. Anthu ambiri m’deralo anati ntchitoyo ikadzatha adzayamba kupita ku misonkhano kuti akaone zomwe zizikakambidwa m’nyumbayo.
Pemphero lathu ndi loti Yehova apitirize kudalitsa mzimu wanu wodzimana pothandiza pa ntchito zomanga Nyumba za Ufumu, kuti dzina lake litamandidwe.
Ndife abale anu,
Ofesi ya Nthambi ya Malawi