Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/07 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 9
  • Mlungu Woyambira April 16
  • Mlungu Woyambira April 23
  • Mlungu Woyambira April 30
  • Mlungu Woyambira May 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 4/07 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira April 9

Nyimbo Na. 201

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenera m’gawo lanu, sonyezani zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya April. M’chitsanzo chimodzi, wofalitsa afunse funso limene adzaliyankhe pa ulendo wobwereza. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa, gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph.15: “Tonse Tingathandize Nawo Kupanga Ophunzira Atsopano.”a Pokambirana ndime 4, pemphani omvera kuperekapo ndemanga za momwe analimbikitsidwira ndi anthu a mumpingo asanabatizidwe. Mungakonzeretu kuti munthu mmodzi kapena awiri adzaperekepo ndemanga.

Mph.20: “Ntchito ya Padziko Lonse Yolengeza za Msonkhano Wachigawo Wakuti ‘Tsatirani Khristu!’”b Pokambirana ndime 3, pemphani omvera kuti asimbe zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pogawira timapepala toitanira anthu ku msonkhano chaka chatha kapena tengani ndemanga za mu Yearbook ya 2007, kuyambira tsamba 7 mpaka 10.

Nyimbo Na. 43 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 16

Nyimbo Na. 161

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph.15: “Lankhulani Mawu a Mulungu Mopanda Mantha.”c Ngati nthawi ingalole, pemphani omvera kufotokozapo malemba amene ali m’nkhaniyi.

Mph.20: “Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?”—Gawo 1.d Ngati nthawi ingalole, omvera aperekepo ndemanga pa malemba onse.

Nyimbo Na. 207 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 23

Nyimbo Na. 215

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pasitetimenti. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenera m’gawo lanu, sonyezani zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa, gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph.15: Kuwala N’kodabwitsa. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2007, tsamba 12 mpaka 14.

Mph.20: “Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?”—Gawo 2.e Malizani ndi kunena mwaumoyo mawu a pa ndime 8.

Nyimbo Na. 172 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 30

Nyimbo Na. 186

Mph.5: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa April.

Mph.10: Zosowa za pampingo.

Mph.30: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2007 Wakuti ‘Tsatirani Khristu!’”f Nkhani yokambidwa ndi mlembi wa mpingo. Limbikitsani onse kuti ayambe kukonzekera msonkhano mwamsanga.

Nyimbo Na. 44 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 7

Nyimbo Na. 164

Mph.10: Zilengezo za pampingo.

Mph.15: Dongosolo Lokhudza Malo Olambirira. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 11.

Mph.20: “Tikapanda Kupeza Anthu Panyumba.”g Yokambidwa ndi woyang’anira utumiki.

Nyimbo Na. 178 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

e Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

f Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

g Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena