Bokosi la Mafunso
◼ Kodi n’koyenera kuti tiziomba m’manja pambuyo pa nkhani iliyonse m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi m’Msonkhano wa Utumiki?
Pamene Mlengi wathu Yehova analenga dziko lapansi, “nyenyezi za m’mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Ana a Mulungu amenewa ndi angelo, ndipo iwo anachita zimenezi pofuna kutamanda Yehova chifukwa cha ntchito yake yodabwitsa yolenga dziko lapansi. Ntchito imeneyi inali yatsopano, ndipo inasonyeza nzeru, ubwino, ndi mphamvu za Mulungu.
Ndi bwino kuti ifenso tiziyamikira abale athu mochokera pansi pa mtima chifukwa cha khama lawo komanso nkhani zimene amakamba. Mwachitsanzo, timaombera m’manja anthu amene amakamba nkhani ndi kuchita zitsanzo pamisonkhano yadera ndi yachigawo. Abalewa amakhala kuti achita khama ndipo athera nthawi yaitali akukonzekera nkhanizi. Tikamaombera m’manja, timasonyeza kuyamikira khama la wokamba nkhani. Komanso timasonyeza kuyamikira malangizo amene Yehova amatipatsa kudzera m’Mawu ndi gulu lake.—Yes. 48:17; Mat. 24:45-47.
Nanga bwanji za kuomba m’manja pambuyo pa nkhani iliyonse m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi m’Msonkhano wa Utumiki? Palibe lamulo loletsa kuomba m’manja ngati munthu wakhudzidwa mtima kwambiri, monga pamene wophunzira wakamba nkhani koyamba m’sukulu. Koma n’zosavuta kuti kuomba m’manja kungokhala mwambo chabe, n’kukhala kopanda tanthauzo. N’chifukwa chake, si koyenera kuti nthawi zonse tiziombera m’manja munthu aliyense akamaliza kukamba nkhani.
Ngakhale kuti sitingaombe m’manja pankhani zambiri m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi m’Msonkhano wa Utumiki, pali njira zina zimene tonsefe tingasonyezere kuyamikira malangizo ndi khama la okamba nkhani. Zina mwa izo ndi kukhala tcheru ndi kumvetsera mosamalitsa okamba nkhaniwo. Ndipo msonkhano utatha, tingapite kwa amene anakamba nkhaniwo ndi kuwayamikira chifukwa cha khama lawo.—Aef. 1:15, 16.