Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/99 tsamba 2
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Tizisonyeza Kuti Ndife Oyamikira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Maphunziro Amene Ufumu Umapereka​—Kuphunzitsa Atumiki a Mfumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 2/99 tsamba 2

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi ndi koyenera kuti omvetsera aziombera m’manja mbali iliyonse ya sukulu yautumiki kapena msonkhano wautumiki?

Omvetsera amene ndi Mboni za Yehova amakhala oyamikira kwambiri. Ndi chinthu chabwino kuti amafuna kusonyeza kuyamikira zimene abale awo achita ndiponso nkhani zimene akamba pa pulatifomu. Masiku ano m’mbali zina za dziko anthu amasonyeza kuyamikira kumeneko mwa kuomba m’manja. Koma kuomba m’manja kuyenera kukhala kwachibadwa, kochokera mumtima. Ndiponso, kaŵirikaŵiri kumasonyeza kuyamikira chinthu chimene chaposa zinthu zina. Ndipo motero, pamisonkhano ikuluikulu, kuphatikizapo misonkhano yadera, pamene mapologalamu apadera akonzedwa ndipo abale athu athera nthaŵi ndi kuyesayesa mowonjezereka pa nkhani zawo, omvetsera amaomba m’manja osati kokha pamapeto pa nkhaniyo komanso mwina pamene nkhaniyo ili m’kati.

Koma kodi zimenezi ziyenera kukhalanso choncho m’Nyumba zathu za Ufumu? Ndithudi sipangakhale lamulo loletsa zimenezi ngati zikuchitika mwachibadwa ndi moyamikira kuchokera pansi pa mtima. Koma kaŵirikaŵiri sitiombera m’manja nkhani zimenezi chifukwa chikhoza kungokhala ngati chizolowezi chabe ndipo motero tanthauzo lake lenileni silingadziŵike.

Komabe, tonsefe tingachite kanthu kena m’Nyumba zathu za Ufumu kuti tisonyeze kuyamikira moona mtima kuyesayesa kwa amene akukamba nkhaniyo; ndiko kukhala tcheru pamene nkhaniyo ikukambidwa, kumamuyang’ana ndi kumaonetsa pankhope pathu kuti tikum’tsatira ndipo tikupindula ndi mfundozo. Ndiponso, kaŵirikaŵiri timatha kulankhula ndi mlankhuliyo ife eni pambuyo pa msonkhanowo, ndi kum’dziŵitsa kuti tinasangalala ndi nkhani yake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena