Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Mutu wa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2009 ndi wakuti “Muonetsetse Kuti Mukukwaniritsa Utumiki,” ndipo wachokera pa Akolose 4:17. Akhristufe sititenga malangizo amenewa mopepuka. Cholinga chathu ndicho kukwaniritsa utumiki wathu mokhulupirika monga mmene Yesu anachitira. (Yoh. 17:4) Nayenso mtumwi Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. Iye anachita khama kwambiri kuti amalize utumiki wake.—Mac. 20:24.
Nkhani ya woyang’anira dera idzasonyeza zimene ofalitsa osiyanasiyana akuchita pothana ndi mavuto amene amakumana nawo muutumiki. Kenako nkhani yakuti “Samalirani Mbewu Zimene Mwabzala” idzasonyeza mmene tingathandizire anthu amene “ali ndi maganizo oyenerera moyo wosatha.” (Mac. 13:48) Mlendo adzayamba kukamba nkhani yofotokoza vesi lililonse la 2 Akorinto 6:1-10, yomwe mutu wake ndi wakuti “Kudzichitira Umboni Kuti Ndife Atumiki.” Masana adzakamba nkhani inanso ya mutu wakuti “Lemekezani Kwambiri Utumiki Wanu.” Tidzalimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani yakuti “Akulu ndi Ana Omwe Amasangalala Kuchita Utumiki” ndi yakuti “Achinyamata Amene Amakwaniritsa Utumiki.” Anthu amene akufuna kusonyeza kudzipereka kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi pa misonkhano imene ikubwerayi ayenera kuuza woyang’anira wotsogolera mwamsanga. Pa misonkhano yathu yonse ikuluikulu timakambirananso nkhani yophunzira ya m’magazini ya Nsanja ya Olonda. Motero, pa tsiku la msonkhano wapadera musadzaiwale kutenga magazini yomwe tidzaphunzire mlungu umenewo.
Poyesetsa kukwaniritsa utumiki wathu, timaonetsetsa kuti zochita zathu zina sizikutidyera nthawi yathu yokwaniritsira udindo umene Yehova waika m’manja mwathu. Malangizo a m’Malemba amene tidzalandire pa tsiku la msonkhano wapadera umenewu, adzatithandiza tonse kumvetsetsa zimene tiyenera kuchita kuti tiike maganizo athu onse pa utumiki wathu. Adzatithandizanso kuona bwinobwino mmene tikuchitira utumiki wathu pofuna kuti tiukwaniritse bwino lomwe.