Kodi Mumagwiritsa Ntchito Nkhani Zonse za M’magazini Yogawira?
1 Mlongo wina atawerenga Nsanja ya Olonda yogawira ya January 1, 2008, anati: “Palibe chifukwa chodikirira kuti ndidzaigwiritsire ntchito muutumiki.” Kodi inuyo munaganizirapo mbali zina za magazini yogawira, n’kuona mmene mungazigwiritsire ntchito muutumiki wakumunda?
2 “Zimene Tikuphunzira kwa Yesu”: Mwina mwaona kuti mbali imeneyi ndi yothandiza kwambiri poyambitsa maphunziro a Baibulo. Ngati panopo simukuona choncho yesani kuwerenga mutuwo kwa mwininyumba, kenako n’kumusonyeza ndime yoyamba kuti aone zimene Yesu ananena pankhaniyo. Munthuyo akasonyeza chidwi, pitirizani kukambirana naye pogwiritsa ntchito mitu ing’onoing’ono yam’nkhaniyi. Kwenikweni mituyi ndi mafunso ochititsa munthu kuganiza. Muuzeni munthuyo kuti apereke maganizo ake pa funsolo. Kambiranani mwachidule chithunzi chogwirizana ndi nkhaniyo kenako n’kuyamba ndime yotsatira. Mungathe kukambirana theka la nkhaniyo paulendo woyamba kenako n’kudzamaliza mbali yotsalayo paulendo wotsatira. Konzekerani zoti mudzapitirize kuphunzirako m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
3 “Chinsinsi cha Banja Losangalala”: Nkhani zimenezi zimatuluka kamodzi pa miyezi itatu iliyonse. Zakonzedwa kuti zizithandiza amuna ndi akazi apabanja komanso makolo, kuti adziwe mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo polimbana ndi mavuto a m’banja. Mungagwiritsirenso ntchito nkhani zimenezi pothandiza anthu amene si mboni kuti apeze nzeru yochokera m’Baibulo.—2 Tim. 3:16, 17.
4 Nkhani za Achinyamata: Nkhani za mutu wakuti “Zoti Achinyamata Achite” zimakonzedwa m’njira yoti zithandize wowerengayo kuganizira mwakuya nkhani inayake ya m’Baibulo. Mungagwiritsire ntchito nkhani zimenezi kuti muthandize achinyamata amene mumakumana nawo muutumiki kuti aone kufunika kophunzira Mawu a Mulungu. (Salmo 119:9, 105) Mukakumana ndi makolo mungakambirane nawo nkhani zokhala ndi mutu wakuti “Phunzitsani Ana Anu.” Nkhani zimenezi zimapezeka m’magazini ya mwezi uliwonse. Ndipo zingathandize ana kutsanzira zinthu zabwino zimene anthu otchulidwa m’Baibulo anachita. Kodi inu mumawerengera ana anu nkhani zimenezi?
5 Nkhani Zina: Magazini ya mwezi uliwonse imakhala ndi nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa.” Nkhani zimenezi zimayankha mafunso amene anthu omwe si mboni angafunse. Mungagwiritsire ntchito nkhani zimenezi pogawira magazini kunyumba ndi nyumba. Amishonale ndi anthu ena amafotokoza bwino mavuto amene akumana nawo muutumiki wawo m’nkhani zakuti “Kalata Yochokera kwa. . . ” Nkhani zimenezi zingathandize anthu achidwi kudziwa kuti uthenga wabwino ukulalikidwa pa dziko lonse lapansi zimene zikusonyeza chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu.—Mat. 24:3, 14.
6 Nkhani zakuti “Yandikirani Mulungu” zimatuluka mwezi uliwonse ndipo zimachokera mu kuwerenga Baibulo kwa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Nkhani zimenezi zingathandize anthu achidwi kufuna kuphunzira za Yehova. Nkhani zakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” zimatuluka kanayi pachaka ndipo zimakonzedwa kuti zithandize anthu kuona m’maganizo mwawo zochitika zotchulidwa m’Baibulo. Zimathandizanso kuti anthu amvetse zimene anthu otchulidwa m’Baibulo anasankha kuchita, mavuto amene anakumana nawo komanso chikhulupiriro chawo.
7 Ndife osangalala kwambiri kuti mwezi uliwonse timalandira magazini ya Nsanja ya Olonda yathunthu yogwiritsira ntchito muutumiki. Tiyeni tiyesetse kudziwa bwino nkhani zonse za m’magaziniwa ndi kuwagwiritsa ntchito bwino muutumiki.