Nkhani Zothandiza mu Utumiki
1. Kodi cholinga cha nkhani zakuti “Kucheza Ndi Munthu Wina” n’chiyani?
1 Nthawi zina mu Nsanja ya Olonda mumakhala nkhani ya mutu wakuti “Kucheza Ndi Munthu Wina.” Nkhani zimenezi zili ndi zolinga ziwiri. Choyamba ndi kufotokoza ziphunzitso za m’Baibulo mogwira mtima ndipo chachiwiri ndi kutithandize kudziwa zimene tingachite kuti tizikambirana mwaluso ndi anthu mfundo za m’Baibulo. (1 Pet. 3:15) Kodi nkhanizi tingazigwiritse ntchito bwanji mu utumiki?
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhani zakuti “Kucheza Ndi Munthu Wina” mu utumiki?
2 Muzigwiritsa Ntchito Nkhanizi mu Utumiki: Muzikhala ndi magazini osiyanasiyana amene ali ndi nkhani zimenezi. Ngati munthu amene mukumulalikira, amene mumaphunzira naye Baibulo kapena munthu wina wakufunsani nkhani inayake yofanana ndi imene inatulukapo m’nkhani zimenezi, mupatseni Nsanja ya Olonda imene ili ndi nkhaniyo ndipo mupempheni kuti mukambirane naye. Ngati mulibe magazini a Nsanja ya Olonda okhala ndi nkhani zimenezi, mukhoza kuchita dawunilodi nkhanizi pa webusaiti ya jw.org/ny.
3. Kodi tingakambirane bwanji nkhanizi ndi munthu mu utumiki?
3 Kodi tingakambirane bwanji nkhanizi ndi munthu? Ena auzapo munthu amene akuphunzira nayeyo kuti aziwerenga mokweza mawu a mwininyumba ndipo iwowo amawerenga mawu a wa Mboni. Njira imeneyi ndi yothandiza kwambiri chifukwa imathandiza munthuyo kudziwa mosavuta zimene timakhulupirira.—Deut. 32:2.
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhani zakuti “Kucheza Ndi Munthu Wina” podziphunzitsa tokha komanso pophunzitsa ena?
4 Gwiritsani Ntchito Nkhanizi kudziphunzitsa Nokha Komanso Kuphunzitsa Ena: Mukamawerenga nkhanizi, muziona malemba, zitsanzo komanso mmene afotokozera mfundo zake. Muzionanso mmene afotokozera nkhaniyo. Kenako yesani kugwiritsira ntchito zimenezo mukamakambirana ndi munthu. (Miy. 1:5; 9:9) Mlongo wina ananena kuti: “Kuwerenga nkhani zimenezi kuli ngati kuphunzira kuchokera kwa mpainiya waluso kwambiri amene amadziwa zoyenera kunena pa nthawinso yoyenera.”
5. Kodi tingathandize bwanji ophunzira Baibulo athu kukonzekera utumiki?
5 Mungagwiritsenso ntchito zitsanzo za m’nkhanizi kuthandiza munthu amene mukuphunzira naye Baibulo kukonzekera zokanena mu utumiki. Mungawerengere limodzi nkhaniyo ndipo wophunzirayo aziwerenga mawu a wa Mboni, inuyo muziwerenga mawu a mwininyumba. Kuchita zimenezi kungathandize wophunzira Baibulo kuti azifotokoza mwaluso kwambiri zimene amakhulupirira. (Akol. 4:6) Nkhani zimenezi ndi njira imodzi imene Yehova akutithandizira kuti ‘tikwaniritse mbali zonse’ za utumiki wathu.—2 Tim. 4:5.